Ulamuliro wa Mulungu - Free Grace Evangelistic Association

Transcrição

Ulamuliro wa Mulungu - Free Grace Evangelistic Association
Ulamuliro wa Mulungu
Pomwe pali Mawu a Mfumu, pamakhala Mphamvu.
Wolemba
I.A. Sadler
Ulamuliro wa Mulungu
Wolemba
I.A. Sadler
Copyright . I. A Sadler 2011.
Lachingerezi linasindikizidwa ndi:
Free Grace Evangelistic Association (Zambia)
P.O. Box 81277, Kabwe, Zambia
Email:[email protected]
ww:freegrace-ea.org
La Chichewa lasindikizidwa ndi:
Assemblies of God Press,5749, Limbe Malawi.
M’malo mwa Free Grace Evangelistic Association (Malawi)
P.O. Box 502, Balaka, Malawi.
Email: [email protected]
Mavesi a Mawu a Mulungu omwe agwiritsidwa ntchito.
Mavesi a Mawu a Mulungu omwe agwiritsidwa ntchito atengedwa mu ‘BUKU
LOPATULIKA NDILO MAWU MULUNGU’ losindikizidwa mu chaka cha 1997. Ili ndi
Baibulo lomwe wolemba anapeza kuti linamasulidwa monga la chingerezi la King
James Version la m’chaka cha 1611, lomwe liri ndi dalitso loposa la Mulungu.
Wolemba wina aliyense yemwe angafune kuti adziwe zambiri za izi angathe
kuwerenga mabuku omwe anasindikizidwa ndi Trinitarian Bible Society (Tyndale
House, Dorset Road, London, SW19 3NN, England), monga buku la ‘The Old is Better’
ndi (Gospel Standard trust), buku lomwe adalemba Dr E. Hills lotchedwa ‘The King
th
James Version Defended’ (4 Edition; ISBN 0-91592300-9).
ZAMKATIMU.
1.Chidziwitso ………………………………………………………………………………….
1
Chiweruzo chiyenera kuyambira mu Nyumba ya Mulungu…….
Kodi liwu lakuti “Ulamuliro” litanthawuza chiyani?.
2.Ulamuliro wa Mulungu monga Mulengi………………………….
4
Pachiyambi Mulungu …… Kuwukira Kotsutsa Ulamuliro wa Mulungu ……
Kutumikira Cholenegdwa kapena Mulengi ….. Amene akonda Mulungu zonse
zithandizana kuwachitira ubwino.
3.Ulamuliro wa Mawu a Mulungu…………………………………...
11
Lamulo Loyera la Mulungu ….. Mphamvu ya Uthenga Wabwino ….. Lalikira Mawu
….. Gwiritsani Mawu Okhulupirira a Chowonadi.
4.Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo………………….
19
Kuwukanso kwa Akufa ….. Chikhululukiro cha Machimo ….. Ulamuliro pa Mpingo
….. Utumiki wa Wukulu wa Kulalikira.
5.Ulamuliro wa iwo Odzozedwa a Mulungu…………………… …
28
Ndondomeko mu Mpingo wa Khristu ….. Ndondomeko mu banja ndi Dziko.
6.Chitsimikizo cha Ulamuliro Wotsiriza wa Mulungu……………
33
Munthu Ayenera Kuyankhapo Mulandu ….. Kubwera kwa Chiwiri kwa Khristu …..
Kumaliza.
Ulamuliro wa Mulungu.
MUTU 1.
CHIDZIWITSO.
Chiweruzo chiyenera kuyambira mu nyumba ya Mulungu.
Mu Chipangano Chakale pa nthawi yomwe Oweruza amatumikira,
timawerenga kuti; “Masikuwa panalibe Mfumu m’Israeli, yense anachita
chomuyenera m’maso mwake”(Oweruza 17:6). Zowonadi tikuziwona izi
zikukwaniritsidwa masiku ano, osakhala mu nyumba za anthu ndi mu dziko,
komanso ngakhale mu mipingo. Wina angathebe kufunsa kuti “Kodi mipingo
ndi Akhristu sanalandire mu masiku ano a Chipangano Chatsopano
vumbulutso la Yesu Khristu, yemwe ali Mfumu ya Mafumu ndi Ambuye Wa
Ambuye?” Inde izi ndi zowona; koma kodi vumbulutso lodalitsikali
lalandiridwa motani? M’mutu kapena mu mtima? Mu thupi, kapena mwa
Mzimu Woyera? Kodi Mulungu akulemekezedwa mu milomo, kapena
mokhulupirika kuchokera mu mtima? Zipatso za uchimo mu masiku athu, ndi
kosasamalira kwa Ulamuliro wa Mulungu ngakhale mu mipingo ya Mulungu
yomwe amavomereza ndi kuchita malamumbiro, zowona zotsimikizika ndi
zakuti ambiri sadziwa Mulungu mu Mzimu ndi chowonadi, kapena ngati
adziwa, abwerera m’mbuyo ndi kuti ali akugona.
Wina angathe kufunsa; “Nanga ndi chifukwa chiyani pali kusasamala
Ulamuliro wa Mulungu ndi kunyoza dzina lake loyera mu dziko komwe kulipo
pa anthu osatembenuka mtima?” Inde, ndipo tifika ku nkhani iyi kutsogoloku.
Nanga ndi chifukwa chiyani dzina la Ambuye linanyozedwa pakati pa
ochimwa? Kodi sichinali chifukwa cha chinyengo cha iwo omwe
amavomereza dzina la Ambuye, omwenso amadzikweza chifukwa cha
chipembedzo chawo ndi kuti ndi obadwa ochokera ku fuko la Abrahamu?
(Aroma 2:17-24). Mtumwi Petro analemba kuti; “Chiweruzo chiyambe pa
nyumba ya Mulungu” (1 Petro 4:17); chomwechonso ndi momwe zikhalire
mu buku ili.
Kodi nanga Ulamuliro wa Mulungu si ukusamaliridwa motere bwanji ndi
ambiri omwe ali Akhristu ovomereza Yesu? Tikuyankha motere kuti ndi
1.
Ulamuliro wa Mulungu.
chifukwa cha kusamvera Mawu a Mulungu. Chifukwa chiyani nanga?
Chifukwa chikondi cha ambiri chazilala. (Mateyu 24;12). Pali chosowa
chachikulu cha chikondi cha uzimu chomukonda Mulungu chomwe chitsikira
kuchoka ku chikondi cha ulemerero cha Khristu kupita kwa ochimwa chomwe
chiwonetsedwa mu moyo Wake, ndi mu imfa Yake ya pa mtanda ndi chomwe
chinavumbulutsidwa kwa ife ndi Mzimu Woyera. Awa ndiye maziko ndi
mphamvu ya kumvera Uthenga Wabwino, “Ngati mukonda Ine, sungani
malamulo anga.” (Yohane 14:15); ndi “Tikonda ife chifukwa anayamba Iye
kutikonda.” (1 Yohane 4:19).
Momvetsa chisoni, ambiri lero sali okhudzidwa ndi nkhani ya kumvera monga
mwa ndondomeko za masiku ano, dongosolo la mipingo, ndi miyambo:
mawonekedwe a uMulungu omwe amalola zambiri za zokondweretsa za
dziko la pansi kuti angathe kumachita popanda kuletsedwa, kudzikundikira
chuma chambiri pa dziko la pansi kuti apititse patsogolo moyo wa wofuwofu.
Koma nanga chikumbu mtima chathu chimatikantha ife? Kodi tiribe makutu
kuti timve chomwe Mzimu akulankhula ku mipingo? Kodi Ambuye Yesu
Khristu sananene kuti; Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga,
adzikanize yekha nanyamule mtanda wake tsiku ndi tsiku nanditsate Ine”
(Luka 9:23). Kodi sitimanthunthumira pa fanizo la wofesa, pomwe Ambuye
anachenjeza za mbewu zomwe zinagwera pa minga?” Ndipo ena ndiwo
akufesedwa kuminga, iwo ndiwo amene adamva mawu, ndipo malabadiro a
dziko la pansi, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina,
zilowamo, zitsamwitsa mawu, ndipo akhala opanda chipatso” (Marko 4:1819). Kodi tikuwumitsidwa mitima lero mu chipembedzo cha ufulu kotero kuti
tikukhala mu moyo wa kuwukira kutsutsana ndi Mulungu, koma tikufunafuna
kuwoneka a chipembedzo chosawonongeka cha chikhristu? Chosowekera
chachikulu chomwe tiyenera kuchifufuza ndi chifundo cha Mulungu mu
chikhulupiliro chowona ndi kulapa.
Kodi liwu lakuti “Ulamuliro” litanthawuza chiyani?
Tisanalowe kwathunthu mu phunziro ili, tiyenera kuti tipeze tanthawuzo la
liwu lakuti “Ulamuliro”. Likutanthawuzidwa mu buku la Mtanthawuza Mawu
kuti “Mphamvu kapena ufulu wakukakamiza kumvera”. ( Concise Oxford
Dictionary, 8th Edition ). Pomwe liwu Lakuti “ulamuliro” likupezeka mu
Baibulo, mawu omwe latanthawuzidwako amamasuliridwanso malo ambiri
2.
Ulamuliro wa Mulungu.
monga “mphamvu” komanso mu malo ena monga “nyonga”, “ulamuliro wa
kukhazikitsa chilamulo”, “ufulu”. Tiyeni tsopano mwapang’ono tiyang’ane ndi
kulingalira pa zitsanzo zochepa.
Khristu anaphunzitsa “monga mwini mphamvu” (Marko 1:22), ndipo “ndi
mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imumvera Iye” (Marko
1:27). Komabe, mawu omwewo mu chiGriki omwenso mu chingerezi
atanthawuza “ulamuliro” mu Marko 1, amatathawuzidwanso “mphamvu” ku
Marko 2:10, pokamba mokhudzana ndi chikhululukiro cha machimo, “mwana
wa munthu ali nayo mphamvu pa dziko la pansi yakukhululukira machimo”.
Mawu a Mulungu awo ali chitsimikizo cha uMulungu wa Khristu, yemwe anali
“Mulungu Iye amene anawonekera m’thupi”. (1 Timoteyo 3:16). Apa
tikuwona kuti pamene tilingalira za ulamuliro wa Mulungu, tiyeneranso
kulingalira za mphamvu yake, nyonga, ufulu ndi kukhazikitsa chilamulo kwake
pa zinthu zonse za pa dziko ndi za kumwamba, za kuthupi ndi za uzimu, kaya
ndi za kanthawi kapena za muyaya. Mulungu ali osiyana ndi ma udindo a
ulamuliro wa umunthu, yemwe, ali bambo ndi mayi ochimwa chabe, ali ndi
malire mu mphamvu ndi chilungamo (monga okhazikidwa ndi kuloledwa ndi
Mulungu). Komabe, mphamvu ya Mulungu iribe malire, ndipo ulamuliro wa
Mulungu ndi wathunthu; palibe chimene chimazemba chilamulo chake.
Ngakhale mfumu yayikulu Nebukadinezara anafikitsidwa pa kuvomereza
Mulungu; “Ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi
nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam’mwambamwamba,
ndi kumuyamika ndi kumuchitira ulemu Iye wokhala chikhalire; pakuti
kulamulira kwake ndiko kulamuilira kosatha, ndi ufumu wake ku mibadwo
mibadwo; ndi okhala pa dziko la pansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye
achita mwa chifuniro chake mkhamu la kumwamba ndi mwa okhala pa dziko
la pansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye,
Muchitanji?” (Daniel 4:34-35).
Ambuye Yesu Khristu wowuka kwa akufa analengeza kwa ophunzira:
“Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine kumwamba ndi pa dziko la pansi”
(Mateyu 28:18). Apa tikuwona kuti mphamvu ndi ulamuliro ndi zimodzi ndipo
zimakhala za mngwiro mwa Khristu Yesu. Ngati ife titamvetsetsa za mphamvu
ndi ulamuliro wa Mulungu m’modzi mwa Atatu, sitikadachitenga
chipembedzo ndi kuvomereza kwa dzina la Ambuye Yesu Khristu kukhala
zinthu za phindu lochepa ndi kusazipatsa ulemu woyenera.
3.
Ulamuliro wa Mulungu.
Anthu osawuka ochimwa oyenera kupita ku gahena, omwe aphunzitsidwa ndi
Mzimu Woyera kuti alilire chifundo, amakokedwa ndi mphamvu ndi
ulamuliro wa ulemerero wa chiyembekezo mu chipulumutso chomwe
mphamvu zonse ndi ulamuliro wonse zigonera mwa Yesu, yemwe
anawakonda iwo nawakhetsera mwazi wa mtengo wapatali. Ali ndi mphamvu
ndi ulamuliro wa kukhululukira machimo awo. Amayenera kungolankhula
mawu, ndipo iwo amapangidwa kukhala angwiro mwathunthu. Analonjeza;
“Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu”. (Mateyu 7:7).
MUTU 2
ULAMULIRO WA MULUNGU MONGA MLENGI.
Pachiyambi Mulungu.
Mitu yoyambirira ya Baibulo ili ndi maziko omwe Mawu Olembedwa onse
amamangidwapo. Masiku ano anthu amanena kuti Mawu Olembedwa
Oyambirira opezeka mu Genesis ali nkhani wamba kapana zizindikiro chabe
osati kuti ndi chowonadi monga momwe zinalembedwera. Ngakhale kuti
chowonadi cha kulenga kwa Mulungu ziri ulamuliro wake monga Mulengi
“chawonekera mkati mwawo pakuti Mulungu anachiwonetsera kwa iwo”.
(Aroma 1:19), komatu munthu wochimwa ali mu kuwukira kowonetsera.
Kukana kwa kusalakwika ndi chowonadi cholembedwa cha buku lonse la
Genesis limalimbana ndi mtima pa za chiphunzitso cha ulamuliro wa
Mulungu, ndi chowonadi chokhazikika chomwe chikhazikitsa umwini
mphamvu wa Mulungu. Mwa tsoka, okhulupirira ndi akhristu ambiri
ovomereza Khristu agwedezeka ndi zomwe a sayansi amenena za kusintha
kwa chilengedwe pakupita kwa nyengo. Ena anayesera kuphatikiza za
kusinthikazi ndi Baibulo, kuyesayesa kuti alumikize zinthu zomwe
sizingalumikizike nazo popeza ndi zosiyana. Ena agwira ntchito kwambiri
pofufuza ndi kuyesa zonse zomwe a sayansi azipeza zomwe ziri zogwirizana
ndi chilengedwe.
Pomwe ziri zosakayikitsa pa kufunika kwa kudziwa za matsutsano zomwe a
sayansi amanena pakukhulupirira za sayansi motsutsana ndi zopanda nzeru
ndi zongoganiza za nkhani ya kusintha kwa zinthu pakupita kwa nyengo,
4.
Ulamuliro wa Mulungu monga Mulengi.
tisowa zoposa ngakhalenso zabwino kwambiri zomwe Akhristu angapereke;
tisowa chikhulupiriro chopatsidwa ndi Mulungu. (Aefeso 2:8). Posakhala
nacho ichi, sitidzakhulupirira moyenera ndi kumvetsa za Ulamuliro wa
Mulungu monga Wolenga. “Ndi chkhulupiriro tidziwa kuti mayiko ndi a
m’mwamba omwe anakonzedwa ndi Mawu a Mulungu, kotero kuti zinthu
zopenyeka sizinapangidwa zochokera mwa zowonekazo. Koma wopanda
chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu
ayenera kukhulupirira kuti alipo ndipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo
akumfuna Iye.”(Ahebri 11:3,6). Chomwecho chikhulupiriro chidza ndi mbiri,
ndi mbiri idza mwa mawu a Khristu.” (Aroma 10:17). Timadalira kwathunthu
pa Mulungu kulankhula mawu a mphamvu mu mitima yathu. Pokhapokha
alankhule, ife timakhala mu mdima. Likhale pemphero lathu ndi chokhumba
chathu kuti Mulungu athe kulankhula monga adachita pa tsiku la kulenga.
“Ndipo anati Mulungu, “Kuyere; ndipo kunayera.”(Genesis 1:3).
Komatu tili nawo Mawu a Mulungu olembedwa akuti ophunzira a Yesu
anadza kwa Yesu napempha kuti awawonjezere chikhulupiriro (Luka 17:5).
Timawerenganso za m’modzi yemwe analira mu kuvutika kwake; “Ambuye
ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga.” (Marko 9:24). Ndipo
Ambuye amamva kulira kwa a umphawi. Chifukwa chake, monga Yesu Khristu
ali “yemweyo dzulo, ndi lero, ndi ku nthawi zonse.”(Ahebri 13:8), tiyeni
potero ifenso tidze kwa Mulungu mogonjera ku chifuniro chake cha
pamwamba. Mwa kulapa, kudandawulira mu dzina la Yesu kuti mphatso ya
mtengo wapatali ya chikhulupiriro ipatsidwe kwa ife mwa Mzimu Woyera.
Titafunafuna ndi mtima wogonja ndi kulapa, apo ndiye pamakhala umboni
weniweni wakuti timalandira ulamuliro wa Mulungu. Komabe, ngati tingafike
pamaso pa Ambuye modzikuza kapena mopanda ulemu, kapena kupemphera
momulamula Ambuye monga ngati tiyenera kena kali konse, apa ndiye kuti
tikukana ulamuliro wa Mulungu monga Mulengi wathu wamphamvu yonse.
Mawu a Mulungu amanena momveka bwino za iwo omwe Ambuye
amawayang’ana mu chifundo. “Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando
wanga wachifumu, ndi dziko la pansi ndi choyikapo mapazi anga;
mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali
kuti? Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi
zinawoneka, ati Yehova; koma ndidzayang’anira munthu uyu amene ali wa
unphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mawu anga.”(Yesaya
66:1-2).
5.
Ulamuliro wa Mulungu monga Mulengi.
Buku la Genesis limayamba ndi kufotokoza za momwe Mulungu analengera
zinthu zonse, zomwe zinakhudza onse Atatu mwa Mulungu kuti analenga
kumwamba ndi dziko la pansi. Dziko la pansi ndipo linali lopanda kanthu,
ndipo mdima unali pamwamba pa nyanja ndipo Mzimu wa Mulungu
unafungatira pamwamba pa madzi. (Genesis 1:1-2). Ndipo keneka
timawerenga za momwe Mulungu analengera china chiri chonse, “ndipo
anati Mulungu;” izi zilankhula za Mawu, Mwana wa Mulungu. Paulo
akulankhula za Mwana; “Amene ali fanizo la Mulungu wosawonekayo,
wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse; pakuti mwa Iye, zinalengedwa
zonse za m’mwamba, ndi za pa dziko, zowoneka ndi zosawonekazo, kapena
mipando yachifumu, kapena ma ufumu, kapena ma ukulu, kapena ma
ulamuliro, zinthu zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye. Ndipo Iye ali
woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana mwa Iye.” (Akolose 1:15-17).
Zowonadi, ulamuliro wa Mawu a Mulungu wakhazikitsidwa kuyambira
pachiyambi pa Mawu Olembedwa, ndipo ali maziko a chowonadi kuyambira
ku Genesis mpaka Chivumbulutso.
Ambuye sanangolenga dziko kokha, komanso dzuwa, mwezi ndi nyenyezi.
“Ndipo Mulungu anati, Pakhale zowunikira pa thambo la kumwamba,
zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku,ndi
zaka; zikhale zowunikira m’thambo la kumwamba; kuti ziwunikire pa dziko la
pansi; ndipo kunatero. Ndipo Mulungu anapanga zowunikira zazikulu ziwiri;
chiwunikira chachikulu chakulamulira usana, chowunikira chaching’ono
chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.”(Genesis 1:14-16). Izi zonse ndi
ntchito za Utatu wa Mulungu, yemwe ali ndi ulamuliro pa dzuwa, mwezi ndi
nyenyezi.
Dziko linalengedwa la ngwiro. Adamu ndi Hava analengedwa opanda chimo,
mu chiyanjano chokwanira ndi Mulungu Mulengi wawo. Ndipo keneka
Mulungu akulengeza ndi Mawu Ake ulamuliro ndi ukulu wake wa munthu pa
zolengewa zina zonse zamoyo za Mulungu. “Mulungu ndipo anadalitsa iwo,
ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchulukane, mudzaze dziko la pansi,
muligonjetse; mulamulire pa nsomba za m’lengalenga, ndi pa za moyo zonse
zakukwawa pa dziko la pansi” (Genesis 1:28). Apa mu Mawu Olembedwa tiri
ndi chokhazikika chomwe chikhazikitsa kuti ulamuliro uli wonse womwe
munthu amagwiritsa ntchito mu chiyanjano ndi Mlengi wake, uyenera
kukhala pa maziko a Mawu a Mulungu. Tiyeni tisayiwale izi mu mpingo wa
6.
Ulamuliro wa Mulungu monga Mulengi.
Khristu. Ngati tifunafuna kuti tigwiritse ntchito ulamuliro motsutsana ndi
Mawu a Mulungu, siwudzapindula pamaso pa Mulungu, ngakhale zitawoneka
ngati ukupindula kwa ka nthawi ku mawonekedwe athu.
Kuwukira kotsutsa Ulamuliro wa Mulungu.
Mitu yotsegulira ya buku la Genesis imalengezanso za udani ndi kutsutsa kwa
Satana kotsutsa ulamuliro wa Mulungu. Pomwe mawu oyamba olankhulidwa
ndi Mulungu mu Genesis ali okhudza za kupereka kwa kuwala, mawu oyamba
a Satana kwa Hava ndi akuti “Eya! Kodi anatitu Mulungu?” (Genesis 3:1).
Kuyambira pa chiyambi pomwe Satana amatsutsa ulamuliro wa Mulungu
umamuyesa munthu kuti awukire natsutsa Mawu a Mulungu nawatsogolera
anthu ku mdima wa uzimu. Pakubzyala mwa anthu chikayiko pa Mawu a
Mulungu, chimagonera pa muzu wa kuwukira kutsutsana ndi Mulungu.
Chiyeso ndi chakuti zambiri zingathe kupezedwa pakudya kwa chipatso
choletsedwa; “mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoyipa.”
(Genesis 3:5). Satana akuyesabe abambo, amayi ndi ana lero pakuwafunsa
Mawu a Mulungu; “Kodi Baibulo lingathedi kutsatiridwa mu zonse zomwe
tichita mu moyo wa masiku ano? Zowonadi pali njira ina yabwino yoposa kuti
tiyitsatsatire? Nyengo zasintha, ndipo sikoyenera kunena kuti ndiwe
wachikale popeza ukutsatira Mawu a Mulungu mosamalitsa? Ngati timakhala
kuti tikuchita monga mwa zabwino kwambiri zomwe tikhumba kuchita,
Mulungu sangakhudzike nazo”. Tiyeni tifufuze chisomo cha Mulungu kuti
tiyankhe Satana, motsatira ndi kudalira pa Ambuye Yesu Khristu. Iye
anamuyankha Satana, “Kwalembedwa, munthu sadzakhala ndi moyo ndi
mkate wokha, koma ndi mawu onse akuturuka m’kamwa mwa Mulungu”.
(Mateyu 4:4). Sitidzakhala ndi moyo ndi ena mwa Mawu a Mulungu ndi ena a
Satana. “Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa Ambuye awiri.”(Mateyu
6:24).
Tiyeni tkumbukire chilango choperekedwa kwa Adamu ndi Hava chifukwa cha
chimo lowukira la kutsutsana ndi Mulungu ndi ulamuliro Wake. Atadya
chipatso choletsedwa, maso anatseguka. Anazindikira kuti anali amaliseche
ndipo anadzipangira zovala za masamba a mtengo wa mkuyu. Chophimba ichi
chomwe anapanga chinali cha nthawi yochepa; sichikadakhoza kuphimba
chimo lawo pamaso pa Mulungu. Adamu ndi Hava anali ndi mantha ndi
kupezeka kwa Mulungu ndipo anabisala. Anathamangitsidwa kuchoka ku
7.
Ulamuliro wa Mulungu monga Mulengi.
Paradiso ndipo iwo pamodzi ndi nthaka zinatembereredwa chifukwa cha
kuwukira kwawo kwa kutsutsana ndi Mulungu. Komatu, Ambuye anali nawo
chifundo, nawapatsa malonjezo a mtengo wapatali a Messiah, mbewu ya
mkazi (Gensis 3:15). Kuwonjezera apo, Ambuye anawawonekera iwo.
“Yehova Mulungu ndipo anapangira Adamu ndi mkazi wake maraya azikopa,
nawaveka iwo” (Genesis 3:21). Mwazi unakhetsedwa kuti Adamu ndi Hava
avekedwe, zomwe zikuyimira mwa chifanizo cha mwazi wokhetsedwa wa
Ambuye Yesu Khristu. Kotero kuti, Yesu yekha ndiye chiyembekezo chathu,
monga tonse mwa chibadwidwe cha umunthu tiri ana amuna ndi akazi a
Adamu ndiponso ochimwitsitsa pamaso pa Mulungu. Yesu Khristu anamvera
Mulungu Atate mwa ngwiro ndipo anachita chilungamo kuti aphimbe
ochimwa umariseche, kuti mwa Mzimu Woyera akhoze kubweretsedwa ku
kulapa ndi kuwalimbikitsa ndi chikondi kuti afikitsidwe kwa Mulungu,
pakukhulupirira pa Iye ndi kudandawulira pa dzina la mtengo wapatali la
Yesu.
Zophunzitsa za chiyambi cha dziko monga mwa kusintha kwa zinthu pakupita
kwa nyengo, komanso za moyo ndi anthu zili chitsutsa cha chindunji ku
ulamuliro wa Mulungu. Chimalimbana ndi kutsegulira kwenikweni kwa ndime
za Mawu Olembedwa, polankhula kwa anthu ambiri kuti, “kodi anatitu
Mulungu?” Sitiyenera kunyengereredwa pa nkhani ngati imeneyi.
Imafunafuna kuchepetsa kusiyana komwe Mulungu anapanga pakati pa
mwamuna ndi makazi, pakati pa anthu ndi nyama. Mu mitu yotsegulira ya
Baibulo, Mulungu anamuyikira mwamuna ulamuliro kuti alamulire mkazi
wake mu chikondi. (Genesis 3:16, Aefeso 5:22-29). Timawerenganso kuti;
“ndipo Yehova Mulungu anawumba munthu ndi dothi la pansi, nawuzira
mpweya wa moyo m’mphuno mwake; munthuyo nakhala wa moyo.”
(Genesis 2:7). Chifukwa cha ichi, bambo aliyense, mayi ndi mwana ali osiyana
ndi nyama pokhala ndi moyo womwe si umafa. Pomwe tingathe kuganiza kuti
tingathe kuthawa ulamuliro wa Mulungu mu moyo uwu, tidzadziwa ndithu za
ulamuliro Wake kwa muyaya, pomwe matupi athu afa ndi pomwe moyo
wathu uwonekera pamaso pa Mulungu woyera kufotokoza mlandu wathu
kwa Iye.
Kutumikira Cholengedwa kapena Mulengi
Tiyeneranso kuti tichenjeze za kuwopsya kwa kutumikira cholengedwa
8.
Ulamuliro wa Mulungu monga Mulengi.
koposa Mulengi. (Aroma 1:25). Izi zikuchuruka masiku ano ndipo zikuchitika
mu njira zosiyana, osati mu dziko mokha, komanso pakati pa akhristu
ovemerezeka, ngakhalenso iwo osamalitsa chikhristu chawo. Izi zimawoneka
mu kukonda ndi kukundika chuma. Tiyenera kuti tifunse: kodi pali
kungokhazikika pa kufunafuna chuma ndi zokondweretsa za dziko lino, ndi
kukana kusiya zokoma za dziko chifukwa cha Khristu, koma pali kufunafuna
kulungamitsa uzimu womwe timawona ngati ndiwotero monga a Farisi.
Tiyeni nthawi zonse tikumbukire kuti Mulungu amawona kudzera mu
chobisalira cha chipembedzo. Adamu ndi Hava adayesa kubisala kwa
Mulungu pa zimene adachita; momwenso ndi momwe adachitira Hananiya
ndi Safira. (Machitidwe a Atumwi 5:1-11). Kodi mitima yathu ndi
yowumitsidwa kutsutsa ulamuliro wa Mulungu kuganiza kuti tikhoza kuti
tikhoza kunyenga Mulungu, pamene ena alephera?
Kulambira ndi kulemekeza cholengedwa koposa Wolenga sizimawoneka mu
chipembedzo cha ochimwa a ‘New Age Movement’ komanso mu zomwe
zimapanga zomwe tikhalamo. Kuwonjeza apo tiyenera kuwachenjeza
Akhristu za zowopsya za kutengapo gawo popanda cholinga chiri chonse mu
zinthu izi, poganiza kuti tikhoza kusewera ndi moto koma osapsya.
Pali mawonedwe osiyana ambiri masiku ano mokhudzana ndi chilenegdwe
chotizinga, zakudya zoyenera, njira za mapangidwe a zakudya ndi
mankhwala. Sichachilendo kupeza Akhristu ovomerezeka akuyika patsogolo
mawonedwe akuti chiri chonse cholengedwa chiri chabwino ndi kuti chiri
chonse chopangidwa ndi munthu chiri choyipa. Poyamba, tiyenera
kuchenjeza kuti izi ndi zotsutsana ndi Mawu a Mulungu. Monga tafotokoza
kale m’mbuyomu, buku la Genesis likufotokoza momveka bwino kuti si
munthu yekha yemwe ali otembereredwa, komanso nthaka ndi chiri chonse
chomwe chitulukamo. (Genesis 3:16-19). Dziko lonse linayipitsidwa ndi chimo
la munthu chifukwa cha kusamvera kwake kwa Mawu a Mulungu. Chachiwiri
ndi chakuti, zambiri za zomwe anthu akuzipanga ndi kuzitsatira ziri nawo
maziko mu zipembedzo za Satana kapena za matsenga, ndiye
tingayembekezere kokondera kwa Mulungu bwanji, koma pokhapokha
titadzipatula kwa iwo? (2 Akoronto 6:14-18). Timachita bwino tikamadziyesa
tokha mosamalitsa mu zinthu izi, kuti miyoyo yathu ikhale pa maziko a Mawu
a Mulungu ndi ku malemekezo ndi ulemerero wa Mulungu. Chifukwa cha ichi,
tisapange chipembedzo chathu kukhala chotiyitanira kuti tibwerere ku thupi.
9.
Ulamuliro wa Mulungu monga Mulengi.
koma kuti tifunefune chisomo cha kubwerera kwa Mulungu monga mwa
Mawu Ake olembedwa komanso osandulika thupi,omwe ndi Ambuye Yesu
Khristu.
Makamaka mu buku la Genesis, zinavumbulutsidwa kuti Mulungu ndiye
Mulengi ndi kuti ali ndi ulamuliro pa chiri chonse chomwe chimachitika pa
chilengedwe Chake. Komabe, mu dziko la anthu akugwa mu uchimo,
chikhalidwe cha kugwa kwathu sichimawona izi. Pomwe tingathe kuzindikira
m’maganizo zomwe Baibulo liphunzitsa, mitima yathu yochimwa
imadzazidwa ndi udani ndi kuwukira chiphunzitso chotere. Pokhapokha
titabadwanso kwatsopano mwa Mulungu Mzimu Woyera, sitingathe
kulandira za chowonadi cha ukulu mphamvu ndi ulamuliro wa Mulungu.
Amene akonda Mulungu zonse zithandizana kuwachitira ubwino.
Kuti okhulupirira awone dzanja la mphamvu la Mulungu mu moyo wake ndi
mu zokumananzo, zimatengera chikhulupiriro chopatsidwa ndi Mulungu.
Poyang’ana ndi diso la umunthu timangowona chipatso cha uchimo ndi
kuwukira kwa munthu mu kuchita choyipa, chiwawa, kukhumba zonyansa ndi
kukonda chuma ndi mphamvu kuti zikupezeka pafupifupi ponse ponse
mdziko la pansi. Komabe, mwa chikhulupiro “timadziwa kuti amene akonda
Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene
ayitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.” (Aroma 8:28). Ngati
mu nthawi ya chinzunzo, zowawa kapena masawutso timawona mwa
chikhulupiriro kuti cholinga chachikulu choposa chiri kukwaniritsidwa ndi
Mulungu, chomwe chidzathera mu chitinthozo ndi chiyanjano chamuyaya ndi
Mulungu mwa Khristu Yesu. Tiyeni potero togonjere ku dzanja la chisomo cha
Mulungu ndi pomwe omutsatira Iye agonjera ku Ulamuliro wa uMulungu
Wake, pokumbukira “chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho”
(Aefeso 2:4). Tiyeni tiwonenso kuti pamene Satana afunafuna kuchita
ulamuliro, Satanayo sangathe kupyola malire omwe Mulungu wamulola.
Chowonadi ichi chavumbulutsidwa mu mitu yoyamba ya buku la Yobu. Tiyeni
potero titonthozedwe mkati mwa mazunzo monga Yobu, popeza mayesero
owopsya awa m’manja mwa Mulungu ndi akuti atiphunzitse kuti tikhoza
kudzimvera chisoni tokha kuti tilape ndi kupereka kwa Mulungu ulemu ndi
ulemerero. Ndipo timawerenga, “Ndipo Yehova anadalitsa chitsiriziro cha
Yobu kuposa chiyambi chake.” (Yobu 42:12).
10.
MUTU 3
ULAMULIRO WA MAWU A MULUNGU.
Lamulo loyera la Mulungu.
Pakulemekeza iwo omwe akufunafuna mowona mtima kuti atsatire Ambuye
tiyeni tiyang’ane nkhani ya J.C. Philpot pomwe analingalira za kusiya mpingo
wa England pa chifukwa cha machitidwe awo osagwirizana ndi Mawu a
Mulungu Olembedwa. Ngakhale kuti amayitanira mowona mtima pa Ambuye
kuti amulanditse iye ndi kumutsogolera. Philpot patapita nthawi
anavomereza: “Ndimayembekezera chozizwa china chake chobwera mkati
chomwe akanamva mawu, kukhala ndi chitsogozo chodabwitsa ndipo pa
kudalira kwa ichi, ndimadikirira pa chomwe Ambuye sanatanthawuze
chimenecho kuti chimuchitikire monga mphatso. “anayenera kuti
abweretsedwe ku kumvera kophweka kwa Mawu a Mulungu ndi mphamvu
ya kutsutsa kwake mu chikumbu mtima chake. Philpot potero anasiya kutsata
zolakwika izi ndi kumutsatira Khristu mu chikhulupiriro ndi chikondi, kuyenda
mu mzimu wowona ndi wa kumvera Uthenga Wabwino.
Kuyambira pachiyambi pomwe pa chilengedwe, timawererenga za mphamvu
ya Mawu a Mulungu, monga momwe tawonera mu mitu ya m’mbuyomu. Pa
ntchito iri yonse yakulenga Baibulo limalemba kuti “ndipo Mulungu anati,”
apatu ndiko kuvumbulutsa za mphamvu ya ulamuliro ya Mawu. Yesero
loyamba la Satana linali lobweretsa chikayiko pa Mawu a Mulungu; chinjoka
chinati kwa Hava “kodi anatitu Mulungu?” Chimo ndi kugwa kwa munthu
m’munda wa Eden kunachitika chifukwa cha kusamvera lamulo la Mulungu.
Mawu Olembedwa amafotokoza kuti panadza mantha mwa munthu kutsatira
kusamvera kwake. Ngati mkwiyo wa chilungamo wa Ambuye
unavumbulutsidwa kwa Adamu ndi Hava, kodi tingaganize bwanji kuti
tidzatha kuzembera ulamuliro Mawu wa Mulungu?
Lamulo la Mulungu loperekedwa kwa munthu lomwe linalembedwa ndilo
Mawu a Mulungu Olemebdwa kudzera mwa mneneri Mose, liri muyeso
wokwanira wa zomwe ziri zonama. Tiri ndi tanthawuzo “chimo ndilo
kusayeruzika.” ( 1 Yohane 3:4 ). Pamene tingathe kupanga zifukwa
11.
Ulamuliro wa Mawu a Mulungu.
m’mawonekedwe a munthu ndi kutsutsa kuchokera mwa ife eni kapena
kunja kwa miyoyo yathu zomwe timalepherera kuchitira chiweruzo
changwiro cha Mulungu, komatu pamaso pa Mulungu sipangakhale kufunsa
za lamulolo, popeza liri la ulamuliro wa Mulungu. Mawu a Mulungu ayenera
kuyima, chimo ndilo kuphwanya kwa lamulo, ndipo liyenera kulandira imfa
yamuyaya.
A Israeli pa phiri la Sinai anapatsidwa lamulo la Mulungu, iwo sanachedwe
kutembenukira ku kupembedza fano. Mose anali atangolandira magome a
malamulo, pomwe a Israeli anali kuvina pamaso pa mwana wa ng’ombe wa
golide (Eksodo 32). Anali ndi ma umboni wokwaniriratu a mphamvu ya
Mulungu ndi nyonga pamaso pawo, komabe mtima wa umunthu wa munthu
wochimwa unali pa udani ndi Mulungu. Mitima yawo inadana ndi njira
yowawa ndi yamayesero, ndipo anafuna kuti apeze njira ina yophweka; ndipo
mitima yathu sikusiyana ndi yawoyo. Mtima wa munthu wokhala monga
mwa umunthu sunasinthike kukhala wabwinopo mwa njira ina iri yonse
kuyambira kuchimwa kwa Adamu, siwunasinthikenso kuchitapo bwino
ngakhale kuyambira nthawi yomwe fano la mwana wa ng’ombe wa gilode
linayengedwa pa phiri la Sinai. “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi
wosachiritsika, ndani angathe kuwudziwa?” (Yeremiya 17:9).
Tikukhala mu tsiku lomwe chikhalidwe chimafananizidwa, kapena
kusiyanitsidwa. Mulingo wa Baibulo wa zomwe ziri zowona ndi zolakwika
umayikidwa pambali, ambiri ndi kumasangalala kuti amphwanya gori lakale
lomwe silingagwirenso ntchito lero komanso chipembedzo chakale
chosagwirizana ndi chikhalidwe cha masiku ano. M’malo mwake ayikapo
mulingo wosunthika wa chiri chonse cha zomwe ambiri azivomereza ndi
kuzilandira. Apa, zomwe ziri zolakwika lero zingathe kukhala zolakwika
mawa, ngati anthu okwanira asintha maweruzidwe awo pa kusinthako.
Komabe, “Mawu a Mulungu akhala chikhalire.“ (1 Petro 1:25). Kugwirizana
kwa anthu ochimwa kutsutsa Mawu a Mulungu, sikungapangitse kuti Mawu a
Mulungu akhale opanda mphamvu.
Dziko losapembedza Mulunguli limawonetsa udani kutsutsa ulamuliro wa
Mulungu mwa kuwukira poyera ndi kusasamalira kwa Mawu a Mulungu;
koma nanga kwa iwo omwe ali Akhristu ovomerezeka? Mu mpingo muli
kuwukira kotichenjerera kopitirira komanso kutsimikizika koposa kotsutsa
12.
Ulamuliro wa Mawu a MUlungu.
ulamuliro wa Mawu a Mulungu. Ena akutsogozedwa ndi chikhalidwe cha
moyo wa masiku ano, ena ndi miyambo ya kale. Mpingo kapena utumiki
ungathe kusankhidwa chifukwa uli wotchuka kapena amasonkhana anthu
ambiri, m’malo mwa “kusankhula kuchitidwa zoyipa pamodzi ndi anthu a
Mulungu.” (Ahebri 11:25). Pali kufufuza kwa Mawu Olembedwa kochepa,
changu cha pa chowonadi cha Mulungu chochepa, palibe kuyamikira kwa
ulemerero wa Mulungu, palibe kukhumba kwa kuwoneka osiyana ndi ena a
mamembala a mu mpingo omwe amalingalira za dziko la pansi. Kuwukira uku
kungathe kuwonekeranso mwa kukakamira ku miyambo, ya banja kapena ya
mpingo. Mayitanidwe ena ali wonse kapena lamulo la m’Baibulo lomwe
lingawayike kunja kwa momwe ziyenera kukhalira amalipewa, ngakhale kuti
liri Mawu omveka bwino a Mawu a Mulungu. Kutakhala kuti “tiyenera
kulindira pa Ambuye”, kapena “sitikutsogozedwa ndi Mzimu za ichi”, ndipo
pa nthawi ino zokoma za dziko la pansi zikukondwereredwa kwathunthu
ngati machitidwe a chipembedzo avomera. Mu zenizeni, izi ndi zowonekera
poyera ndi kufuna dala kwa kusamvera kwa ulamuliro wa Mulungu.
Mphamvu ya Uthenga Wabwino.
Monga momwe Mawu a Mulungu alengeza za uthunthu wa mulingo wa
kukhoza ndi kulakwa, momwenso alengeza za njira ya chipulumutso kudzera
mwa Yesu Khristu ndi ulamuliro womwewo. Mawu Olembedwa
amakhazikitsa uMulungu Wake, umunthu Wake wa chiyero, kumvera kwa
ngwiro Kwake ku lamulo loyera la Mulungu ndi imfa yake ngati mwana wa
nkhosa wa Mulungu, kupereka nsembe ya ngwiro ya machimo a Mpingo
wowona wa Mulungu pa mtanda, ndipo kenaka kuwukanso kuchokera ku
imfa kuti tikhoze kukhala ndi moyo mwa Iye.
Chowonadi chokha mwa Yesu Khristu, Mawu a Mulungu a muyaya, ndi
chomwe chimamasula ochimwa otsutsidwa pansi pa lamulo la Mulungu
(kuphatikizapo ochimwa achipembedzo) kuwachotsa ku ukapolo wa chimo,
imfa ndi gahena. Ambuye anati, “Ngati mukhala inu m’mawu anga muli
akuphunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira chowonadi ndipo
chidzakumasulani.”(Yohane 8:31-32). Iyi ndi ntchito yodalitsika ya Mulungu
Mzimu Woyera kutsogolera ku chowonadi chonse. (Yohane 16:13). Apatu
tiyenera kukhala mu moyo wopemphera kwambairi kuti Mzimu athe
kutitsogolera, kutikoka ndi kuchita Mawu a Mulungu. Sangalephere
13.
Ulamuliro wa Mawu a Mulungu.
kuthandiza wochimwa wosawuka yemwe adzipereka yekha ku kuchita lamulo
lake. Tisowa kumasulidwa ndi Mzimu Woyera kuchoka ku mzimu wonyansa
womwe umanong’oneza kuti “aunyinji ayenera kukhala wokhoza” ndi
chiwanda cha mtundu wake womwewo chomwe chimati “muyenera
kusamalira miyambo yathu.” Koma ife tiyenera kunena kuti, “Mulungu akhale
owona, ndipo anthu onse akhale onama.” (Aroma 3:4). Tiyeni tipemphere
kuti tidzazidwe ndi changu cha pa Mawu a Mulungu, chowonadi chake,
ulemerero Wake, ndi kugonjera mokondwera ku ulamuliro Wake.
Mawu a Mulungu amalengeza ndi ulamuliro momwe Mpingo uyenera
kuyendetsedwera komanso za moyo wa wokhulupirira aliyense. Komabe izi
siziri monga mwa mphamvu za ulamuliro. Mphamvu zimadzera ku ntchito
zodalitsika za Mzimu Woyera. “Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo
mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse,
ndi mafano anu onse. Ndipo ndidzakupatsani mtima watsopano, ndi kulonga
m’kati mwanu mzimu watsopano, ndipo ndidzachotsa mtima wa mwala
m’thupi, ndi kukupatsani mtima wa mnofu. Ndipo ndidzayika mzimu wanga
m’kati mwanu, ndi kukuyendetsani m’malemba anga ndi kuwachita” (Ezekiel
36:25-27).
Ndiye kuti, ulamuliro ndi mphamvu za Mawu a Mulungu pa wokhulupirira
zimachitika ndi kukakamiza kokoma kwa Mzimu kuvumbulutsa chikondi
chotifera cha Khristu. Kawiri mu makalata omwe atumwi analembera
mipingo mu Baibulo, wolemba wodzozedwa amatifikitsa pa “kulingalira Iye.”
(Ahebri 12:3) kuti “tikhale nawo mtima mkati mwathu umene unalinso mwa
Khristu Yesu.” (Afilipi 2:5), potikumbutsa za chikondi cha Mulungu
chowonetsedwa mwa Yesu Khristu. Kudzera mu mphamvu ya kuwuka kwake
kwa Khristu ndi momwe tikhala ndi moyo ndi kutumikira Mulungu mu moyo
watsopano, ndi kubereka zipatso zopereka ulemerero wa Mulungu kuyenda
kudzera mu chiyanjano cha uzimu ndi Khristu (Yohane 15). “Pakuti chikondi
cha Khristu chitikakamiza” (2 Akoronto 5:14).
Lalikira Mawu.
Talankhula za mamembala a pa mpingo, nanga wolalikira bwanji? Kodi
chitsogozo ndi chiphunzitso amazifunafuna kuti? Kodi ndi kuchokera ku
wailesi ya kanema, kapena ku uthenga wojambulidwa womwe akuwonera
14.
Ulamuliro wa Mawu a Mulungu.
wina akulalikira? Kapena amatenga zophunzitsa kuchokera ku zomwe
anaphunzira ku sukulu ya Mawu a Mulungu (Ya Ubusa)? Kodi wolalikira
akungofuna kutengera ena omwe akuchita bwino ndi kuti anthu
amuyamikire.” Komabe, mtumwi Paulo analengeza, “Kapena kodi ndifuna
kukondweretsa anthu? Ndikhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala
kapolo wa Khristu.” (Agalatiya 1:10).
Mlaliki wa Uthenga Wabwino ayenera kulengeza “uphungu wonse wa
Mulungu”. (Machitidwe a Atumwi 20:27). Uphungu wa Mulungu
umavumbulutsidwa kwa munthu mu Mawu a Mulungu owuziridwa omwe
apatsidwa kwa ife mu Buku Lopatulika, liwu liri lonse linawuziridwa ndi
Mulungu ndipo liri ndi ulamuliro. (2 Timoteo 3:14-17). Kudzera mu Mawu a
Mulungu Olembedwa ndi momwe timakhala ndi vumbulutso lathunthu la
Mulungu, maweruzo Ake ndi njira Yake ya chipulumutso mwa Khristu Yesu.
Chifukwa cha ichi Paulo anamulimbikitsa Timoteo kuti, “Lalika mawu” ndi kuti
“Uchite changu kudziwonetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wa ntchito
wopanda chifukwa cha kuchita manyazi wolunjika nawo bwino mawu a
chowonadi.” (2 Timoteo 4:2, 2:15). Kulalikira kwa Mawu a Mulungu uku
sikuyenera kukhala mwa njira iri yonse ya chiphunzitso chowuma, kapena mu
chidziwitso cha kuphunzira, koma kuchokera mu kulengeza kokhulupirika
kwa Mawu a Mulungu pamodzi kudzoza kwa Mzimu Woyera, “Pakuti
Uthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m’mawu mokha, komanso mu
mphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera ndi m’kuchuruka kwakukuru.” (1
Atesalonika 1:3).
Mtumiki wolalika Uthenga Wabwino ayenera kukhala mboni ya zomwe iye
akudziwa monga munthu yemwe ali pansi pa ulamuliro wa uMulungu.
Mtumiki Yohane analengeza mwa kudzozedwa kwa Mulungu, “Chimene
chinaliko kuyambira pa chiyambi, chimene tidachimva, chimene
tidachipenyerera, ndipo manja anthu adachigwira cha mawu a Moyo, (ndipo
moyowo unawonekera, ndipo tidawona, ndipo tichita umboni, ndipo
tikulakirani moyo wosathawo, umene unali kwa Atate, nuwonekera kwa ife);
chimene tidachiwona, ndipo tidachimva tikulakirani inunso, kuti inunso
mukayanjane pamodzi ndi ife, ndipo chiyanjano chathu chirinso ndi Atate,
ndipo ndi Mwana wake Yesu Khristu.” (1 Yohane 1:1-3). Kulephera apo,
sipadzakhala ulamuliro wa uzimu mu utumiki. Anthu angathe kuyesera
zomwe zimakondweretsa kuti akole ku kugwiritsa ntchito mphamvu zawo pa
15.
Ulamuliro wa Mawu a Mulungu.
anthu afowoka, kuti akakamize kapena kugometsa, kutenga mwa
kutamandira, koma mtumiki yemwe amagwiritsa ntchito njira za ku thupi
kuti awonetse ulamuliro wake pa anthu kapena kuti mpingo wake ukule mu
chiwerengero (ngakhale atakhala kuti akuwoneka kuti akupambana pamaso
pa anthu) iye ali mu kuwukira kotsutsa ulamuliro wa Mawu a Mulungu.
Gwiritsitsani Mawu Okhulupirika a Chowonadi.
Okhulupirira owona ndiponso enieni amasocheretsedwa ndi kuti mipukutu
ina yakale (yomwe inakanidwa ndi mipingo pakupita pa nyengo kuti
ndiyosadalirika) iyenera kugwiritsidwa ntchito tsopano pomanganso Mawu
Olembedwa ndi kuti azigwiritsidwa ntchito.
Njira imodzi yalutha yomwe Satana akuyigwiritsa ntchito mu mibadwo
yatsopano ndiyo kubweretsa Mawu a Mulungu olembedwa omwe ali
otanthuwuzidwa molakwitsa. Izi zimakopa mwamitundu yisiyana kwa
chikhumbo cha munthu wakugwa cha mabuku wamba ndi njira zomwe
ambiri azitsatira za matanthawuzidwe a Baibulo. Kawirikawiri zolinga zawo
posindikiza bodza lawo zimakhala mwa zokhumba za wosindikiza kuti apeze
phindu lalikulu kwa Akhristu okhala mwa umunthu, kapena kuchokera mu
zolakwitsa kapena ophunzira a Mawu a Mulungu omwe akupititsa patsogolo
mphekesera chabe. Pofunafuna kuti akhazikitse zikhulupiriro zawo pa
mipingo. Kulephera apo, matanthawuzidwe ena amachokera mu
mawonekedwe osatsogozedwa, akuti zowonadi za uzimu zingathe
kuphunzitsidwa mwa kuphweketsa chilankhulo choperekedwa ndi
kuwuziridwa ndi Mulungu.
Munthu akapita ku nyumba yogulitsa mabuku angathe kupezako mitundu
yambiri ya matanthawuzidwe a Baibulo, onsewo kumatsimikizidwa kuti ndi
Mawu a Mulungu, komatu mu malo ambiri samagwirizana lina ndi linzake.
Ambiri a iwo ali mboni zonama zomwe zikufesa chisokonezo pakati pa
mipingo ndi okhulupirira osakhazikika omwe sangazindikire bwino lomwe
kuti Mawu a Mulungu eni eni ndi ati. Woyambitsa chisokonezo chotere si
Mulungu, koma Satana yemwe kuyambira mu Eden wakhala akufunafuna
kuti anong’oneze kuti. “kodi anatitu Mulungu?” Chotsatira chotsiriza ndicho
zomwe tichitira umboni lero, pomwe wowerenga akusiyidwa pa malo akuti
asankhe matanthawuzidwe omwe iye akukonda kwambiri, osati kuti agwe
16.
Ulamuliro wa Mawu a Mulungu.
modzichepetsa pansi pa ulamuliro ndi mphamvu ya Mawu a Mulungu.
Zokhotetsa za masiku anozi zachepetsa ulamuliro wa Mawu mu mitima ndi
miyoyo ya Akhristu ovomerezeka ambiri.
Zikadakhala zochitika bwino kupitirira cholinga kuchikwaniritsa mu buku
laling’ono ili, kuti tilowe mu kukambirana za matanthawizidwe asiyana siyana
a Baibulo. Komabe, mu chilankhulo cha chingerezi, Baibulo la ‘King James
Version’ lomwe linatanthawuzidwa mu chaka cha 1611, ndilo
lotanthawuzidwa mokhulupirika kwambiri lomwe lisunga Malembo a
mipukutu yomwe inali yoyambirira kulembedwa, lomwe linatanthawuzidwa
ndi anthu akhulupirika ndi a uzimu; kusonyeza kuti mu chingerezi
limalandiridwa ngati Mawu a Mulungu olembedwa. Ziri zofunika ku mbali ya
moyo wa uzimu wa mipingo kuti Mawu a Mulungu osadetsereredwa
akugwiritsidwa ntchito, kuwerengedwa.
Komabe, tiyeni tichenjezedwe kuti mwina tingagwiritse ntchito Baibulo
lotanthawuzidwa mokhulupirika la Mawu a Mulungu, koma ndi
kusakhulupirika mu njira yomwe tikuwagwiritsira ntchito Mawu
Olembedwawo. Kodi tikuwamasulira Mawu Olembedwa monga mwa
miyambo yathu? Ndiye kuti Mawu a Mulungu ali kupereka ulemu ku
miyambo yathu ndi kuti tiri mu chiyanjano ndi Afarisi, osati Mwana wa
Mulungu. Nthawi iri yonse yomwe sitizindikira Mawu Olembedwa tiyeni
titsatire ndondomeko ya uMulungu yomwe Mawu Olembedwa
amamasulidwira. Monga Mulungu Mzimu Woyera anawuzira Mawu
Olembedwa a Mullungu, kodi Mzimuyo sadzavumbulutsira chowonadi kwa
okhulupirira odzichepetsa omwe afunafuna kuwunika ndi chitsogozo mwa
pemphero? (Luka 11:13). Tiyeni tipemphere kuti Mulungu Mzimu Woyera
atsegule mitima yathu kuti tilandire Mawu ndi kutipatsa mphamvu kuti
tiyende mu mawuwo. Pali kusowekera kwakulu mu mpingo masiku ano kwa
pemphero lowona la munthu, kuwerenga ndi kufunafuna Mawu.
Ngakhale pali zolimbana ndi ulamuliro wa Mulungu wa Mawu a Mulungu.
Malonjezo a Muluggnu ndi okhazikika, “Atero Yehova, Kumwamba ndi
mpando wanga wachifumu, ndi dziko la pansi ndi chiyikapo mapazi anga;
mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali
kuti? Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi
zinawoneka, Ati Yehova; koma ndidzayang’anira munthu uyu amene ali wa
17.
Ulamuliro wa Mawu a Mulungu.
umphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mawu anga.” (Yesaya
66:1-2).
MUTU 4
ULAMULIRO WA KHRISTU MONGA MUTU WA MPINGO.
Kuwukanso kwa Akufa.
Talingalira za ulamuliro wa Mawu a Mulungu Olembedwa, ndipo tsopano
tiyenera tilingalire za ulamuliro pa mpingo wa Ambuye Yesu Khristu, Mawu
osandulika thupi. (Yohane 1:1-14).
Ambuye Yesu Khristu, pakuyamba pa utumiki wake wa dziko la pansi,
anabwera ku Yerusalemu ndi kolowa mu Kachisi. Mmenemo anapeza ogula,
ogulitsa ndi osintha ndalama amitundu yosiyana siyana. Mu mkwiyo wake
wolungama anayeretsa mpingo ku zinthu zoterezi. “Ndipo pamene adapanga
mkwapulo wazingwe, anaturutsa onse m’Kachisimo, ndi nkhosa ndi ng’ombe;
nakhuthula ndalama za osinthawo, nagubuduza magome, nati kwa iwo
akugulitsa nkhunda, chotsani izi muno; musamayesa nyumba ya Atate wanga
nyumba ya malonda.” (Yohane 2:15-16). Ayuda ndipo anafuna kuti Yesu
apereke chizindikiro cha ulamuliro Wake wakuchitira zinthu zotere. Yesu
anayankha , “Gwetsani Kachisi uyu, ndipo ndidzamumanganso mu masiku
atatu.” Yesu amalankhula za kachisi wa thupi Lake, kulengeza za chitsimikizo
cha ulamuliro wake pa mpingo kuti unayenera kukhala imfa Yake ndi
kuwukanso kwa akufa. Kuwonjezera apo, kuwukanso kwa akufa kwa Yesu
Khristu kuli chitsimikizo chakuti ali Mwana wa Mulungu. Paulo analemba kuti
Iye amene anatsimikizidwa ndi mphamvu kuti ndiye Mwana wa Mulungu
monga mwa Mzimu wa Chiyero, ndi kuwuka kwa akufa.” (Aroma 1:4). Ayuda
a chipembedzo sakadakhoza kulandira kapena kukhulupirira izi, ngakhale kuti
mwachangu ndi khama amalondoloza miyambo yawo ya chipembedzo.
Koposatu makamaka kwa Ayuda osakhulupirira, koma kodi tiri ndi makutu
kuti “timve chomwe Mzimu alankhula ku mipingo?” (Chivumbulutso 2:29).
Ambuye Yesu Khristu wowuka kwa akufa ndi wopatsidwa ulemerero
anawonekera kwa mtumwi Yohane pa chisumbu cha Patmo ndi kulengeza ndi
18.
Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo.
ulamuliro za chiweruzo chake changwiro pa mipingo isanu ndi iwiri ku
mipingo ya ku Asia. Zinthu izi zinalembedwa kuti zitilangize ndi kutichenjeza,
ndipo mipingo siyidzathawa ziweruzo zolungama za Mutu wamkulu wa
Mpingo pokhapokha ngati tilandira ndi kumvera chilimbikitso chochokera
kwa Khristu mwini, “potero chita changu, nutembenuke mtima.”
(Chivumbulutso 3:19). Paulo anachenjeza mpingo wa ku Ahebri; “Penyani
musakane wolankhulayo.” (Ahebri 12:25).
Mtumwi Paulo akulembanso kwa Aefeso za mapemphero ake owona mtima
kuti apatsidwe nzeru, chidziwitso ndi kuzindikira kwa “chiyembekezo cha
kuyitana kwake nchiyani, chiyaninso chuma cha ulememrero wa cholowa
chake mwa oyera mtima, ndi chiyani ukuru woposa wa mphamvu yake ya
kwa ife a mphamvu yake yolimba, imene anachititsa mwa Khristu, m’mene
anamuwukitsa kwa akufa, namkhazikitsa pa dzanja lake la manja
m’zakumwamba, pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu,
ndi ufumu, ndi dzina liri lonse lotchedwa, si m’nyengo yino ya pansi pano
yokha, komanso mwa iyo ikudza; ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake,
nampatsa Iye akhale mutu pamtu pa zonse, kwa Eklesia amene ali thupi lake,
mdzazidwe wa Iye amene adzaza zonse mu zonse.” (Aefeso 1:18-23).
Chikhululukiro cha Machimo.
Tikapitirirabe kuwerenga kalata ya Paulo yolembera mpingo wa ku Efeso,
timawona kuti, “Khristu ndiye mutu wa Eklesia; ali yekha Mpulumnmutsi wa
thupilo” (Aefeso 5:23). Khristu monga Mutu wa Mpingo ali nawo ulamuliro
ndi mphamvu kukhululukira chimo. Pomwe adabweretsa kwa Yesu munthu
yemwe ankadwala matenda a manjenje, amene mwa chikhulupiriro
adamugoneka pa mapazi a Yesu, Ambuye anati “Mwana, machimo ako
akhululukidwa. Koma anakhalapo ena a alembi akuganizira mu mitima
mwawo, Munthu amene atero bwanji? Achita mwano; akhoza ndani
kukhululukira machimo koma m’modzi; ndiye Mulungu?” (Marko 2:5-7).
Keneka Yesu anawonetsera mwa kuchiritsa mozizwitsa munthu ameneyu,
kuti Ali nayo mphamvu pa dziko ya kukhulukira machimo ndi kuti Iye
zowonadi ali Mulungu wowonetsedwa mu thupi (1 Timoteo 3:16).
Zowonadi zake ndi zakuti Yesu Khristu ndi Mulungu, Mfumu ya Mafumu
ndiponso Ambuye wa Ambuye. Mwa chisomo Iye amachitachita mwa
19.
Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo.
mphamvu imeneyi ndi ulamuliro umenewu, monga Mutu wa Mpingo, kuti
awombole ochimwa kudzera mu mwazi Wake wa mtengo wapatali.
Okhulupirira owona mtima ali ogulidwa ake. “Kapena simudziwa kuti thupi
lanu liri kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa
Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Pakuti munagulidwa ndi mtengo
wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m’thupi lanu,’ (1
Akorinto 6:19-20). Izi zimalankhula za ntchito ya Khristu ya chiwombolo
kudzera mu mwazi wake wokhetsedwa kuti apulumutse ochimwa,
kuwabweretsa iwo kwa Iye kudzera mu ntchito yodalitsika ya Mzimu Woyera
ndi kuti awasunge mu chikondi pansi pa ulamuliro Wake.
A Yuda osakhulupirira, sanamvere Uthenga Wabwino, koma anali osamvera
ku mawu ndi ntchito ya Ambuye Yesu Khristu (Aroma 10:16). Ngakhale kuti
“Anawaphunzitsa monga mwini mphamvu.” (Mateyu 7:29), anapitirirabe
kudzilungamitsa okha pansi pa chilamulo. Mtumwi Paulo analemba za
momwe Ambuye anamumasulira Iye (Khristu), wosati wakukhala nacho
chilungamo changa cha m’lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha
Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro.” (Afilipi
3:9).
Chipulumutso
sitimachipeza kudzera mumphamvu yathu ndi ufulu
wakusankha, “koma onse amene anamlandira Iye, kwa iwotu anapatsa
mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu akukhulupirira dzina lake;
amene sanabadwwa ndi mwazi, kapena ndi chifuniro cha thupi, kapena ndi
chifuniro cha munthu, koma cha Mulungu.” (Yohane 1 :12-13). Mu ndime iyi
ya Mawu Olembedwa mawu ayambirira omwe anatanthawuzidwa
“mphamvu”. Omwe tawonanso m’mbuyomu kuti akutanthawuzanso “ufulu”
kapena “mwayi”. Apatu ndiye kuti ndi kuchokera kwa Khristu Mutu wa
Mpingo yemwe anakwaniritsa lamulo loyera la Mulungu, kuti wochimwa
wobwera kwa Yesu amapatsidwa mphamvu ndi mwayi mwa Mzimu Woyera
kudzera mu chikhulupiriro kuti angathe kufikira chipulumutso chachikuru
chotere. Izi zikuwoneka kuti zikufanizidwa ndi nkhani ya Yakobo kulandira
dalitso pa doko la Yaboki, “ndipo analimbana naye munthu kufikira
mbandakucha. Ndipo pamene anawona kuti sanamlaka, anakhudza nsukunyu
ya ntchafu yake; ndipo nsukunyu ya ntchafu yake ya Yakobo inaguluka,
pakulimbana naye. Ndipo iye anati Ndileke ndimuke, chifukwa kuli kucha.
Ndipo Yakobo anati, Sindidzakuleka iwe kuti umuke, ukapanda kundidalitsa
20.
Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo.
ine. Ndipo iye anati kwa Yakobo. Dzina lako ndani? Nati iye, Yakobo. Ndipo
nati dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israeli, chifukwa unayesana
naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.” (Genesis 32:24-28).
Mwa manyazi tiyenera kuyang’ana kuchepa kwa mapamphero opambanitsa
omwe akuchitika mu masiku ano, kaya ndi pa gulu ngakhale mwa mseri.
Kawirikawiri mu Mawu Olembedwa timawerenga za ulamuliro ndi mphamvu
za mapemphero a aneneri, monga Mose, Eliya ndi Elisha. Mphamvu imeneyi
simachokera mwa iwo eni, koma kwa Mulungu. Ambuye Yesu Khristu
akuvumbulutsa chinsinsi cha pemphero. “Ngati mudzapempha Atate kanthu
adzakupatsani inu m’dzina langa” (Yohane 16:23). Mukakhala nacho
chikhulupiriro monga kambewu ka mpiru, mudzati ndi phiri iri, senderapo
umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo kulibe kanthu kadzakulakani
kosachitika.” (Mateyu 17:20) “Ndipo pamene Iye anadziyitanira ophunzira
ake khumi ndi awiri, anapatsa iwo mphamvu (Ulamuliro) pa mizimu yoyipa,
yakuyiturutsa, ndi yakuchiza nthenda iri yonse ndi zofoka zonse.” (Mateyu
10:1). Tikubwerezanso kunena kuti mphamvu ndi ulamuliro uwu zimachokera
kwa Khristu, inde Khristu yekha basi, ndipo imadziwidwa pomwe titsatira
mayitanidwe a uMulungu wake. Mphamvu iyi singapezeke mwa njira ina iri
yonse ngakhale kugulidwa ndi ndalama. (Machitidwe a Atumwi 8:18-21).
Tiyeni mowona mtima tidandawulire Ambuye kuti mwa chisomo atipatse
mzimu wowona wa pemphero la kulimbana ndi kuwonjezera kwa
chikhulupiriro monga mu masiku otsiriza timapempherera zinthu zomwe
zavumbulutsidwa bwino lomwe mu Mawu a Mulungu.
Ulamuliro pa Mpingo.
Monga Ambuye Yesu Khristu ali Mutu wa Mpingo, kotero ali ndi ulamuliro wa
uMulungu pa miyoyo ndi mayitanidwe kuyambira a mpingo komanso
wokhulupirira ali yense pa yekha omwe amapanga mpingo. Ali ndi ulamuliro
kuyitana ndi kutsogolera monga Iye afuna; koma palibe kuyitana kapena
kutsogozedwa ndi Mulungu komwe kungakhale kotsutsana ndi Mawu a
Mulungu owuziridwa Olembedwa. Sipadzakhala kusiyana pakati pa
chitsogozo cha Mzimu Woyera ndi Mawu a Mulungu Olembedwa ndi
osandulika thupi; ndipo mu zinthu zonse Mzimu ndi Mawu zinakwaniritsa
zolinga za muyaya za Atate. “Pakuti pali atatu akuchita umboni, Mzimu, ndi
21.
Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo
madzi, ndi mwazi, ndipo iwo atatu ali m’modzi.” (1 Yohane 5:8).
Tisowa kudzichepetsa ndi kugonjera, kulindira pa kuyitana kwa Ambuye;
ndipo pomwe kwalandiridwa, tisowekeranso kwambiri kuti timvere ndi
kuyenda mu mayitanidwewo. Zingathe kukhala kuti mayitanidwe omwe
takhala tikuwafunafuna, kapena njira yomwe takhala tikuyilingalira. “Pakuti
maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu siziri njira zanga, ati
Yehova. Pakuti monga kumwamba kuli kutari ndi dziko la pansi, momwenso
njira zanga ziri zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana
maganizo anu.” (Yesaya 55:8-9). Kapena siyidzakhala njira yophweka
“tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisawutso zambiri” (Machitidwe
a Atumwi 14:22). “ndipo onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa
Khristu Yesu, adzamva mazunzo.” ( 2Timoteo 3:12). Koma ndi njira yomwe
imatitengera ku moyo wosatha. Ali ndi mphamvu ndi ulamuliro kuti
atisamalire ife kuchokera kwa adani athu onse, kuchokera ku chimo,
chiwonongeko, imfa ndi gahena. Adzatipyoletsa mayesero athu onse.
Pamene anthu a Ambuye apatuka pa njira ya chowonadi, kaya ndi mu
kusamvera, kunyada, kusasamala, kapena kupereka ulemu ku miyambo ya
makolo athu, Ambuye ali ndi ulamuliro wa uMulungu kuti apereke chilango.
Komatu kupereka mwambo uku kumachitidwa mu chikondi ndipo ku ubwino
wa ife, ndiponso chiri chikole cha chikondi chake. Pakuti iye amene Ambuye
amkonda amlanga, kulanga uku ndi “kukatipindulitsa, kuti tikalandire nawo
pa chiyero chake. Chilango chiri chonse pakuchitika, sichimamveka
chokondweretsa, komatu chowawa, koma chitatha, chipereka chipatso
chamtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.
Mwa ichi limbikitsani manja ofowoka, ndi mawondo olobodoka, ndipo
lambulani misewu yolunjika yoyendamo mapazi anu.” (Ahebri 12:6-12).
Utumiki wa Wukulu wa Kulalikira.
Atawuka kwa akufa Ambuye, chomwe chiri chitsimikizo chachukulu cha
ulamuliro wa uMulungu wake, Ambuye anawonekera kwa akuphunzira ake.
Analankhuila mawu achitonthozo ndi mtendere; ndipo izi zinadza ndi
mphamvu mu mitima yawo. Ndipo anawapatsa ntchito yomwe imadziwika
kuti Utumiki Wawukulu yakulalikira Uthenga Wabwino. “Mukani ku dziko
lonse la pansi lalikirani Uthenga Wabwino kwa olenegdwa onse.” (Marko
22.
Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo.
16:15). Ku Mateyu 28 kunalembedwanso kuti Ambuye anatuma ophunzira
Ake kuti “aphunzitse anthu a mitundu yonse” ndi ku Machitidwe a Atumwi
mutu woyamba, Ambuye atawuka kwa akufa anati, “mudzalandira mphamvu
Mzimu Woyera atadza pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu,
ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko la
pansi” (Machitidwe a Atumwi 1:8). Polingalira za Utumiki Wawukulu,
ziphunzitso zathu zonse ziyenera kukhala pa maziko a Mawu Olembedwa;
osawonjezepo kena kali konse kapena kuchotsa pa Mawu a Mulungu.
Pomwe pali kuyenera kutsindika kuti palibe munthu yemwe angathe
kulalikira mowona kapena molunjika, pokhapokha ngati watumidwa ndi
Mulungu (Aroma 10:15), ndi mayitanidwe a mipingo yonse pamodzi komanso
okhulupurira ali yense payekha payekha kuti akhale mboni za Khristu mu
tsiku la mdima ndi loyipa. Tiyeni tifunefune chisomo cha Mulungu kuti tichite
motero mu mzimu wowona wa chikondi, mwawuthunthu kutsatira Mawu a
Mulungu. Pomaliza, tiyeneranso kuwona kuti pali kusiyana pakati pa Utumiki
Wawukulu ndi zizindikiro zomwe Ambuye analonjeza kuti zidzatsatira
malingana ndi chifuniro chake cha uMulungu.
Pomwe membela wokondedwa kapena mlaliki akufuna kuti anyamuke
kuchoka pa mpingo, angathe kupereka mawu a malangizo otsanzikana,
kapena amakhala mawu awo omaliza. Kufunika kwakukulu kumaphatikizidwa
ku mawu otere, ndipo mamembala a tchalitchi kawirikawiri amakumbutsidwa
patapita nthawi za uphungu wa woyera mtima, yemwe wachoka. Ngati zinthu
zimakhala choncho, ndi chifukwa chiyani pali kupereka ulemu kochepa ku
mawu otsiriza a Yesu Khristu, amene ali Mutu wa Mpingo? Tisanazilingalire
moposera izi, tiyeni tiwerenge nkhani yathunthu ya Utumiki Wawukulu
womwe unaperekedwa mu Uthenga Wabwino wa Mateyu. “Ndipo Yesu
analankhula nawo, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba
ndi pa dziko la pansi. Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu
yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate ndi la Mwana ndi Mzimu Woyera;
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu, ndipo
onani Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi
ya pansi pano.” (Mateyu 28:18-20). Njira yomwe inalembedwa mu Mawu a
Mulungu yomwe ndi yotumizira kwa anthu njira ya chipulumutso
simangophatikiza ku kulakira, komanso Mawu a Mulungu Olembedwa
(Yohane 20:31) pamodzi ndi umboni wa munthu payekha. Kuchokera ku
23.
Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo.
Mateyu 28, timawona chifukwa chake chenicheni cho “mukira ku dziko lonse
la pansi ndi kuphunzitsa anthu a mitundu yonse” kuti zigonera mu mphamvu
ndi ulamuliro wa Khristu; ndi kuti mu kumuka monga mwa lamulo lake. Iye
amatipatsa lonjezo lodalitsika la kupezeka Kwake kufikira ku mapeto a
nthawi. Komabe, ena amapanga chiphunzitso cha umwini mphamvu wa
Mulungu mu chipulumutso kudzilungamitsa kwawo pa kusasamalira za
Utumuki Wawukulu, posinkhasinkha kuti chipulumutso ndi cha Mulungu ndi
kuti sikuli kwa munthu kuti akhoza kuyika dzanja lake mu nkhani iyi. Koma
pomwe Mulungu Mzimu Woyera akutsogolera tidzapangidwa kugonjera ndi
kumvera pomutsogolera ku mayitanidwe a Mawu a Mulungu. Ubale,
mphamvu ndi ulamuliro wa Khristu ziri zifukwa zenizeni zotipangitsa kumvera
Utumiki Wawukulu. “Pakuti mawu a mfumu ali ndi mphamvu ndipo ndani
anganene kwa Iye, Kodi uchita chiyani? (Mlaliki 8:4). Tiyeni tisamale pa
kusamvetsa chisoni Mzimuyo kudzera mu kusamvera.
Ena amawona kulakwitsa kwa Utumiki Wawukulu, ndi kudzibweza kuchoka
ku malingaliro a “ntchito ya umishonale.” Komabe, Utumiki Wawukulu siwa
kwa anthu a mitundu yonse okha, komatu kwakukulu imayenera kulalikira
kokhulupirika pamodzi ndi kuphunzitsa kwa “zinthu zonse zomwe
ndinakulamulirani; kulankhula mwa mawu ena, uphungu wonse wa Mulungu
wovumbulutsidwa mu Mawu a Mulungu ngati tingalalikira kapena
kuphunzitsa gawo la uphungu wa Mulungu wa kwa anthu a mitundu yonse,
makamakatu uku ndi kuwupotoza uphunguwo.
Sizirinso gawo la Utumiki Wawukulu kugwiritsa ntchito zisudzo, masewero,
ziwonetsero za zidole, ziwonetsero za nyimbo, ndi zina zambiri. Sizirinso za
Mawu Olembedwa kuti mowona ndi mosaledzera “kupereka” Uthenga
Wabwino, ngati zaperekedwa kwa omvera kuti iwo okha ali ndi mphamvu
mwa iwo okha kuti apulumutsidwe. Mawu Olembedwa amanena momveka
bwino kuti “Lalikira Uthenga Wabwino.” Anthu angathe kutchula kulalikira
“chopusa”, koma Mtumwi Paulo analemba: “pakuti popeza mnzeru ya
Mulungu dziko la pansi, mwa nzeru yake, silinadziwa Mulungu, chidamkonda
Mulungu kupulumutsa okhulupirirawo mwa chopusa cha kulalikira. Ndipo
popeza Ayuda afunsa zizindikiro, ndi Ahelene atsata nzeru, koma ife tilakira
Khristu wopachikidwa, kwa Ayudatu chokhumudwitsa, ndi kwa amitundu
chinthu chopusa.” (1 Akorinto 1:21-23).
24.
Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo.
Mfundo zotsatira za zomwe tangolankhula zokhudza kulakira ziyenera
kugwiritsidwa ntchito chimodzimodzi ku magawo ena a Utumiki Wawukulu,
zomwe ziri kuphunzitsa ndi kuchitira umboni. Ziyeneranso kutengedwa
chimodzimodzinso malingana ndi ndondomeko monga mwa Mawu
Olembedwa osati monga mwa dziko la pansi.
Tiyeninso tifotokozere momwe Mulungu amalemekezeredwa malingana ndi
Utumiki Wawukulu mwa umboni wa okhulupirira, omwe ngakhale
sanayitanidwe kuti alalikire pagulu, amachitira umboni za mphamvu ya
Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu kudzera mu ntchito za chikondi. Tiri ndi
zitsanzo zomwe ziri mu Mawu Olembedwa. Mwa chitsanzo pali Dorika,
yemwe ankasamalira mu njira zambiri amayi amasiye. (Machitidwe 9:39); tiri
ndi Gayo yemwe anali nazo ntchito za chikondi ndi kulandira ndi kusamalira
alendo (3 Yohane 1-6); ndiponso pali Febe “ndiye mtumiki wa mkazi wa
Mpingo wa Ambuye wa ku Kenkreya; kuti mumlandire iye mwa Ambuye,
monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m’zinthu ziri zonse
adzazifuna kwa inu, pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe.
Mulankhule Priska ndi Akula, antchito anzanga mwa Khristu Yesu. (Aroma
16:1-3).
Mu tsiku la zokhumudwitsa zambiri, ena amawona kuchepa kwa anthu
m’mipingo ndi kutsekedwa kwa mipingo kukhala chinthu chomwe sitingathe
kuchipewa, chifukwa masomphenya a Utumiki Wawukulu atayidwa. Izi ndi
zochitika zomwe zimachitika mobwerezabwereza, chifukwa Mawu a Mulungu
amanena kuti, “Popanda chivumbulutso anthu amasawuka.”(Miyambo
29:18). Fanizo la ndalama zomwe zinaperekedwa kwa antchito (Luka 19:1127) limafotokoza za momwe Mbuye analamulira aliyense wa iwo “Chita
nazoni malonda kufikira ndidzabweranso.” Mbuye atabwera, anafunsa za
momwe aliyense “anapindulitsira pa kuchita malonda.” Ena anachita khama
pa kuchita monga mwa lamulo la Mbuye uja, ngakhale panali udani wa
“mbadwa” kwa Mbuyeyo. Komabe, kapolo m’modzi anabisa ndalama imodzi
ndipo analandira mkwiyo, osati matamando ochokera kwa Mbuye. Tiri ndi
fanizo lofanana ndi lomweli la matalente mu Mateyu 25. Mafanizo awiri
onsewa amapereka chenjezo la mphamvu kutsutsana ndi kubisa kwa chuma
chachikulu cha chowonadi cha Mulungu. Tiyeni potero tiwonetse kulapa
kochokera pansi pa mtima penipeni pa zinthu izi, pofunafuna chisomo cha
Mulungu mowona mtima kuti chikhulupiriro chathu chiwonjezeredwe.
25.
Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo.
Mulungu Mzimu Woyera yekha, mwa kuyankha kwa pemphero ndi kulapa
kwenikweni, angathe kutiwombola ku machitidwe awa. Kudzera mu
pembedzero ndi pemphero mu dzina la Yesu Khristu kuti mipingo komanso
munthu aliyense payekha afunefune mwa Mzimu Woyera chisomo, nzeru
kulimba mtima ndi madanga a kuchitira umboni kwa Uthenga Wabwino
malingana ndi Mawu a Mulungu mu mzimu wa chikondi ndi kudzichepetsa.
Tiyeneranso kulingalira za funso iri: kodi Uthenga Wabwino uyenera
kulalikidwa kuti. Ndipo kwa yani? Mu mpingo kapena m’kachisi mokha?
Timawerenga mu Marko kuti ophunzira “anaturuka, nalalikira ponse ponse,
ndipo Ambuye anchita nawo pamodzi, natsimikiza mawu ndi zizindikiro
zakutsatapo.” (Marko 16:20). Kotero kodi tingayemebekeze “zizindikiro
kutsatira” ngati tisankha malo omwe Uthenga Wabwino uyenera kulalikidwa?
Chimodzimodzinso, Mawu a Mulungu amafotokoza momveka bwino kuti
Uthenga Wabwino uyenera kulakidwa kwa “olengedwa onse”, ngakhale kuti
tachenjezedwa kuti ambiri sadzamva, chifukwa mitima yawo
ndiyowumitsidwa. Komabe, sitiyenera kuponyera ngale kwa nkhumba kuti
ziponderezedwe pansi pa phazi. (Mateyu 7:6); kuyenera kuti maweruzidwe
abwino ndi chitsogozo cha Mzimu kunena mowona ndi zomwe tisowa.
Pomaliza, zakhazikitsidwa mu Mateyu 28:19-20 ndi Mawu ena Olembedwa za
masakramenti a ubatizo wa okhulupirira ndi chakudya cha Ambuye chomwe
chimatchedwanso Mgonero. Tiyenera kukumbukira kuti izi zinakhazikitsidwa
ndi Ambuye mwini kuti zitsatidwe ndi okhulupirira onse, omwe
amabweretsedwa ndi Mzimu Woyera ku kulapa ndi chikhulupiriro mwa
Khristu. Tiyeni tilingalire kuti tanthawuzo lochokera mu buku la Mtanthawuza
Mawu lotanthawuza mawu a sakramenti ndi akuti “dongosolo kapena
chokhazikitsidwa ndi ulamuliro.” Pokha pokha pamene tiyenda mwa
chikhulupiriro mu kumvera Khristu, ndi pomwe Mulungu amalemekezedwa
ndi kupatsidwa ulemerero kudzera mwa kuvomereza kwathu kwa dzina Lake.
Pomwe pali zambiri zomwe zikananenedwa, tiyenera kumaliza ndi chosowa
chofunika kwambiri cha kutsatira Khristu mwa chikhulupiriro, mu chikondi
kwa Iyeyo monga Mutu Wamkulu wa mpingo. Ngati mu kudzera mu
kusamvera tikuyenda mutsutsana ndi Mulungu, kapena ngati sitikuyenda mu
malamulo a Mulungu kudzera mu ulesi, kuwopa munthu, miyambo kapena
chifukwa china chiri chonse, titsimikizidwe za ichi, sitidzapita patsogolo
26.
Ulamuliro wa Khristu monga Mutu wa Mpingo.
kapena kupindula. Tiyeni tiyike pa mtima Mawu a Khristu pakupemphera
mowona mtima kuti tilandire chisomo Chake ndi kuti tilape mowona mtima.
Lonjezo lake liri ndi ulamuliro wa uMulungu ndi lotsimikizika, “Ndidzalowa
kwa iye, ndipo ndidzadya naye ndi iye ndi Ine” (Chivumbulutso 3:20)
MUTU 5
ULAMULIRO WA IWO ODZOZEDWA A MULUNGU.
Ndondomeko mu Mpingo wa Khristu.
Khristu monga Mutu wa mpingo anadzoza atumwi ndi kuwatuma “ndipo
pamene Iye anadziyitanira ophunzira ake khumi ndi awiri, anapatsa iwo
mphamvu ndi ulamuliro pa mizimu yoyipa yakuyiturutsa, ndi yakuchiza
nthenda iri yonse ndi zofowoka zonse.” (Mateyu 10:1). Atakwera Khristu
kupita ndi kulowa kumwamba, atumwi anagwiritsa ntchito ulamuliro mu
mpingo wa Khristu. Ulamuliro uwu unatengedwa kwa Khristu mwini mwa
Mzimu Woyera, ndipo mwakulamulidwa ndi chikumbu mtima chawo kuti
athe kugwiritsa ntchito ulamulirowo mwa chikondi ndi mwakumvera Khristu.
(2 Akorinto 12:15).
Mtumwi Petro chimodzimodzinso akulemba zokhudza iwo omwe ali ndi
ulamuliro mu mpingo wa Mulungu. “Akulu tsono mwa inu ndiwadandawulira,
ine mkulu mzanu ndi mboni ya zowawa za Khristu, ndinenso wolawana nawo
ulemerero udzavumbulutsikawo; Wetani gulu la Mulungu liri mwa inu, ndi
kuliyang’anira, osati mokangamiza, koma mwa ufulu, kwa Mulungu, osatsata
phindu linyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a
udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo. Ndipo pakuwonekera Mbusa
wa mkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota.” (1 Petro 5:1-4).
Nkhani yomwe ikufanizidwa apo ndi ya mbusa yemwe ali pansi pa mbusa
wamkulu yemwe akusamalira gawo la busa la Khristu lomwe Iye, monga
“Mbusa wa mkulu wazipereka kwa iwo. Chisamaliro ichi chiyenera kuchitika
mu chikondi; monga Khristu anawakonda iwo, kuwonetsera mwa miyoyo
yawo ndi utumiki chikondi cha Mulungu. Monga Khristu alamulira pa Mpingo
mu chikondi, momwenso mbusa wamng’ono alamulire pa busa lomwe iye
wapatsidwa kulisamalira mokhulupirika ndi kulamulira mu mphamvu ya chikondi.
27.
Ulamuliro wa iwo Odzozedwa a Mulungu.
Kenaka Petro akulembera kwa iwo omwe ali mamembala a pa busa la
nkhosa; “Momwemonso anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu
muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza,
koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.” (1 Ptero 5:1-4). Paulo
akulembanso, “Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindira moyo
wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati
mwachisoni; pakuti ichi sichikupindulitsani inu”. (Ahebri 13:17).
Tikufunafuna kuti tikhazikitse mfundo zoyenera kutsatiridwa apo,
posamalitsa kuti mipingo yosiyana iri ndi ndondomeko zawo zawo za
mawonekedwe a mpingo, ndi omwe ali ndi ma udindo osiyanasiyana ali ndi
mayina omwe adatchulidwa m’Baibulo (mwa chitsanzo mbusa, bishopu,
dikoni, kapena mkulu wa mpingo). Ngakhale ziri chomwecho, momwe
ndondomeko ya dongosolo iri, liyenera kukhala mogwirizana ndi Mawu
Olembedwa.
Komabe,
tikhoza
kupeza
pomaliza
zotsatira
zingapo
apa.
Sitingayembembekezere kuti tiwone kutuluka kapena kupindula mu mpingo
ngati iwo omwe ali pa ma udindo a mpingo alamulira mu nkhanza, kukonda
chuma kapena mosakhudzika ndi anthu, poganiza kuti ali “ufulu wa
uMulungu” wa mtundu wina wake wakuti akhoza kulamulira mu mpingo
monga momwe angafunire ndi kuti azingomvera ziri zonse iwo akulamulira.
Pakuchita motero, alibe ulamuliro wa Mulungu mwa njira ina iri yonse.
Kapenanso tisayembembekeze kupindula pakudzikuza kuti titsutse iwo omwe
ali ndi ulamuliro monga mwa Mawu Olembedwa pa ife. Chifukwa chake, kaya
tiri pa gome, pa desiki kapena kumvera otilalikira, pali kusowekera kwa
kuyenda kwa wina ali yense payekha ndi Khristu kuti pamenepo pakhale
chiyanjano chowona ndiponso umodzi mu mpingo. “Koma ngati tiyenda
m’kuwunika, monga Iye ali m’kuwunika, tiyanjana wina ndi mzake, ndipo
mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.” (1
Yohane 1:7).
Nanga tinena kuti chiyani za mipingo imene malo a ma udindo amakhala
opanda anthu kwa nthawi yopanda malire eni eni? Kodi tiyembekezere
dalitso la Ambuye pomwe ndondomeko ya kumwamba yavumbulutsidwa mu
28.
Ulamuliro wa iwo Odzozedwa a Mulungu.
Mawu a Mulungu sinatsatiridwe? Titenge monga chitsanzo mpingo wopanda
mbusa. Nthawi ina kamodzi Khristu anawona unyinji wa anthu; Iye
“anagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa;
ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Marko 6:34). Kotero kuti
mipingo isowekera kukhala ndi mbusa kuti aphunzitse Mawu a Mulungu ndi
kusamalira nkhosa za pa busa. Ngakhale mu zinthu za ku thupi, nkhosa
zopanda mbusa zingathe kusokera mosavuta, kukhala ndi njala,
kusocheretsedwa kapena kugwidwa ndi nkhandwe ndi mimbulu.
Nanga tingayembekeze bwanji mpingo kuti upindule pomwe palibe mbusa,
kapena kufunafuna mwa pemphero ndi chikhumbokhumbo chakukhala ndi
m’modzi. Zingathe kunenedwa kuti, “tiyenera kukhutira ndi zinthu zomwe tiri
nazo”, koma Mawu Olembedwa awa otengedwa m’Baibulo okhudzana ndi
kukwaniritsidwa ndi chuma cha dziko la pansi popewa kukonda chuma, osati
kukwaniritsidwa ndi Mawu Olembedwa komwe kukuchitika mu mpingo.
Wina angathe kunena kuti, “mpingo wakhala wopanda mbusa kwa zaka
zambiri ndipo Ambuye watithandiza kufikira lero.” Inde, izi zisonyeza kuleza
mtima ndi chifundo cha Mulungu, koma sitiyenera kuwona kuti zikhoza
kumakhala choncho. Zinanenedwanso kuti, “ngati titakhala ndi mbusa,
sitingathe kumva atumiki osiyanasiyana omwe ife timakondwera nawo”; inde
dziko la pansi limati “kasinthasintha ndiko kukometsa kwa moyo,” koma izi
siziyenera kutsatiridwa ndi mpingo. Chowonadi chomveka bwino chochokera
mu Mawu Olembedwa ndi ichi, “Ndipo ndidzakupatsani inu abusa monga
mwa mtima wanga, adzakudyetsani inu nzeru ndi luntha.” (Yeremiya 3:15).
Kafukufuku wosabisika wa Mawu a Mulungu amawonetsa kuti udindo wa
mbusa uli gawo la ndondomeko ya Mawu Olembedwa (1 Timoteyo 3, Tito 1,
Machitidwe a Atumwi 20:17-38). Ngati titafunafuna machitidwe a mtundu
wina, tiri pa kuwukira kotsutsana ndi Khristu monga Mutu wa Mpingo.
Pamene pali mphatso za ma utumiki ndi mayitanidwe osiyana omwe
Mulungu mu mphamvu yake amapereka, monga awo a abusa, aphunzitsi ndi
alaliki (Aefeso 4:11), udindo wa abusa unakhazikitsidwa ndi Mulungu kuti
upindulire ndi kumangirira mpingo. Izi zimanyalapsyidwa ndi kunyozedwa
kotitengera ife ngozi.
Ndondomeko mu Banja ndi Dziko.
Mawu a Mulungu amakhazikitsa ndondomeko yomveka bwino m’banja,
29.
Ulamuliro wa iwo Odzozedwa ndi Mulungu.
yomwe yagonera pa chikondi cha nsembe cha Khristu ku Mpingo, ndi
kumvera kwa Mpingo kwa chikondi kwa Khristu. “Akazi inu, mverani amuna a
inu eni, monga kumvera Ambuye. Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi,
monganso Khristu ndiye mutu wa Eklesia, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.
Komatu monga Eklesia amvera Khristu, koteronso akazi amvere amuna awo
m’zinthu zonse, Amuna inu, kondani akazi anu monganso Khristu anakonda
Eklesia, nadzipereka yekha m’malo mwake.” (Aefeso 5;22-25).
Nanga ndi chifukwa chiyani chikhalidwe cha masiku ano chatenga malo
kwambiri mu mpingo kwa abambo ndi amayi kupanga zowinda zofanana
zomwezo, ndi kusiya chowinda cha kumvera m’malo mwa mayi? Kodi nanga
iwo omwe avomereza kutsatira Mawu a Mulungu amakakamira pa zowinda
zomwe zigwirizana ndi zikhulupiro za ku dziko pa kuzifananiza? Mu nijira
zambiri izi zikuchitika kudzera mu umbuli wa Mawu Olembedwa. Koma nanga
mayitanidwe okhulupirika a mtumiki wa Uthenga Wabwino? Mwambo
wodalitsa ukwati wosatsatira Mawu Olembedwa sungathe kuchitika popanda
mbusa kuwalora okwatitsidwa kuti achite malumbiro osokonezedwa
amenewa. Ziri m’manja mwa mbusa kuti pakhale kuyakhapo mulandu wa
ukulu pamaso pa Mulungu, osakhala pa mwambo wodalitsa ukwati
wokhawo, komanso kuti aphunzitse uphungu onse wa Mulungu asanadalitse
ukwatiwu.
Mu ndondomeko ya ngwiro ya Mulungu ya banja, kumvera kwa mkazi
kumalimbikitsidwa ndi chisamaliro cha chikondi cha mwamuna mwa nsembe
kwa mkazi wake. Mwamuna ali ndi ulamuliro wa Mawu a Mulungu
wakulamulira pa nyumba yake, koma ziyenera kuchitika mwa chikondi.
Mwamuna sayenera kulamulira mwa nkhanza, koma yemwe alamulira
modzichepetsa. Munthu wa Mulungu m’modzi (yemwe anapita ku
ulemerero) anafotokoza moyenera ndi mwachidule kuti fungulo la
kukhutitsidwa ndi chisangalalo mu banja ndi mawu akuti “chimwemwe”.
Anatenga mawu atatu a chingerezi omwe atanthawuzidwa chimwemwe mu
Chichewa, ndipo anati ngati Yesu ali woyambirira, munthu wina (mwamuna
kapena mkazi) ali wachiwiri, ndi iweyo ndi wachitatu; apo ndiye kuti
padzakhala chimwemwe m’banja, “musachite kanthu monga mwa chotetana,
kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa
mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini; munthu yense asapenyerere
zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mzake. Mukhale nawo
30.
Ulamuliro wa iwo Odzozedwa a Mulungu.
mtima mkati mwanu umene unalinso mwa Khristu Yesu.” (Afilipi 2:3-5).
Momwenso, Mawu a Mulungu alamulira ana kuti “amvere akuwabala mwa
Ambuye; pakuti ichi ndi chabwino. Lemekeza atate wako ndi amayi ako.”
Makolo alamuliridwa kuti asakwiyitse ana awo koma kuti awalere iwo mu
m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” Antchito ayenera kumvera
ambuye awo; “monga kumvera Khristu,” ndi ambuye ayenera kusamala
kusawawopsyeza, “podziwa kuti Ambuye wawo ndi wanu ali M’mwamba.”
(Aefeso 6:1-9).
Komabe, lero tikuwona kuswedwa kwa kulemekeza kwa ulamuliro
wokhazikitsidwa ndi Mulungu. Izi zikuwoneka m’banja, makamaka mwa
kufunafuna kwa zinthu kosafuna kukanizidwa kwa onse awiri mwamuna ndi
mkazi kuti atsatire ntchito zawo, kuwasiya ana kuti aleredwe ndi kukulitsidwa
mu malangizo ndi maweruzo a wayilesi ya kanema, foni ya m’manja, intaneti,
kapena za makhalidwe onyansa ndi osapembedza Mulungu. Zikuwonekanso
mu mwano womwe antchito amawuwonetsa ku ulamuliro wa ma bwana
awo.
Mu dziko, Mawu a Mulungu amalamulira kuti mbadwa ziyenera kupereka
ulemu woyenera kwa iwo omwe ali mu ulamuliro. Mtumwi Paulo analemba;
“Anthu onse amvere ma ulamuliro a akulu, pakuti palibe ulamuliro wina
koma wochokera kwa Mulungu. Kotero kuti iye amene atsutsana nawo
ulamuliro, akaniza choyikika ndi Mulungu; ndipo iwo akukaniza; adzitengera
kulanga. Pakuti mafumu sakhala owopsya ntchito zabwino koma zoyipa.
Ndipo ufuna kodi kusawopa ulamuliro? Chita chabwino, ndipo udzalandira
kutama m’menemo; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe
zabwino. Koma ngati uchita choyipa, opatu, Pakuti iye sagwira lupanga
kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera
chilango wochita zoipa. Chifukwa chake, kuyenera kuti mukhale omvera, si
chifukwa cha mkwiyo wokha, komanso chifukwa cha chikumbu mtima.
Pakuti chifukwa cha ichi mupatsanso msonkho pakuti iwo ndiwo atumiki a
Mulungu akulabadirabe chinthu chimenechi. Perekani kwa anthu onse
mangawa awo, msonkho kwa eni ake msonkho; kulipira kwa eni ake
kulipidwa, kuwopa kwa eni ake kuwopa, ulemu kwa eni ake ulemu.” (Aroma
13:1-7).
31.
Ulamuliro wa iwo Odzozedwa a Mulungu.
Kuwonjezera apo, tikuwuzidwa kuti tiyenera kupempherera iwo omwe ali ndi
ulamuliro pa ife. “Ndidandawulira tsono, poyambayamba, kuti achitike
mapembedzo, mapemphero, mapambedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu
onse, chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro, kuti m’moyo
mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m’kulemekeza Mulungu, ndi
m’kulemekeza monse. Pakuti ichi ndi chokoma ndi cholandirika pamaso pa
Mulungu Mpulumutsi wathu.” (1 Timoteyo 2:1-3).
Komabe, anthu ambiri mu dziko lino amakhala. Osati pansi pa atsogoleri
osapembedza kokha, koma pansi pa iwo omwe amazunza okhulupirira
owona. Kotero ndi momwe adachita ndi Paulo mu nthawi yake. Nanga
tingatenge kuti Mawu Olembedwa kuti tithe kunena kuti “ayi” kwa iwo omwe
ali ndi ulamuliro pa ife mu zinthu zokhudza za dziko la pansi? Mawu a
Mulungu akutipatsa ife zitsanzo zomveka bwino mu buku la Danieli. Ana a
chiHebri ndi Danieli yemwe nthawi zonse adawonetsa ulemu woyenera ndi
kumvera mafumu a ku Babulo ndi Peres. Komatu, pomwe anayitanidwa kuti
achite chomwe chinali choletsedwa ndi Mulungu (kulambira mafano) ndi kuti
asiye kupemphera kwa Mulungu, motsimikiza mtima ndi mwa ulemu iwo
anamvera malamulo a Mulungu, osati malamulo a mfumu ya dziko la pansi.
Osasamalira zomwe munthu akadakhoza kuchita motsutsana nawo, Ambuye
anayima pambali pawo ndi kuwawombola. Pali phunziro iri la ife lero
kuchokera mu Mawu Olembedwa.
Mwa tsoka ku Ulaya, tikuwona kuti kuwukira kukunka kukulira kulirabe kwa
ana kutsutsa ulamuliro wa makolo awo, mbadwa za dziko kutsutsa atsogoleri
omwe aperekedwa kwa iwo, antchito kutsutsa owalemba ntchito, akazi
kutsutsa amuna awo, kawiri kawiri pansi pa mbendera ya “ufulu wa
chibadwidwe”. Koma mpingo wa Mulungu wovomereza Khristu wayamba
kutsatira zinthu izi, tingayembekezere bwanji kuti dziko lisinthe kukhala
labwino? Mulungu ali wokwiya mwa chilungamo; ndipo adzafunsa anthu kuti
ayankhepo chifukwa cha zinthu izi, komatu makamaka kuchokera kwa ife
amene tiri ndi Mawu Ake Olembedwa pamaso pathu, koma kuti sitidayende
mu Mawuwo. Koposa kotani nanga kuti adzafuna kwa iwo omwe alalikira
zolakwitsa mu mipingo, ndipo ndi utumiki wosakhulupirika okana poyera kuti
njira za Mulungu ziri zangwiro!
Chisokonezo mu mipingo, m’banja ndi mu dziko zingathe kukonzedwa
32.
Ulamuliro wa iwo Odzozedwa a Mulungu.
mowona ndi mphamvu ya Mzimu Woyera. Pali kusowekera kwakukuru kwa
pemphero kuti Uthenga Wabwino udze ndi mphamvu ndi moyo.
MUTU 6
CHITSIMIKIZO CHA ULAMULIRO WOTSIRIZA WA MULUNGU.
Munthu Ayenera Kuyankhapo Mulandu.
Ngakhale kuti timasunga mwa mphamvu za umunthu chiphunzitso cha
umwini mphamvu wa Mulungu, momwe munthu wakugwa wasandulitsidwa
bwinja “pakufa ku zolakwa ndi uchimo; ndi kufunika kwa ntchito ya Utatu wa
uMulungu mu chipulumutso. (Aefeso 1 ndi 2), momwemonso mwa mphamvu
timasunga kufotokoza kwa zomwe tachita kwa anthu onse kwa Mulungu.
“Pakuti mkwiyo wa Mulungu wochokera Kumwamba, unawonekera pa
chisapembedzo chonse ndi chosalungama cha anthu, amene akanikiza pansi
chowonadi mchosalungama chawo; chifukwa chodziwika cha Mulungu
anachiwonetsera kwa iwo. Pakuti chilengedwere dziko la pansi zawoneka
bwino zosawoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi uMulungu wake;,
popeza sazindikira ndi zinthu zolenegdwa, kuti iwo adzakhale opanda mawu
akuwiringula, chifukwa kuti, ngakhale anadziwa Mulungu, sanamchitira
ulemu wakuyenera Mulungu, ndipo sanamyamika; koma anakhala opanda
pake m’maganizo awo, ndipo unada mtima wawo wopulukira”. (Aroma 1:1821). Mtumwi Petro analemba kuti, “masiku otsiriza onyoza ndi kuchita
zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, ndi kunena, Liri kuti
lonjezano la kudza kwake? Pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse
zikhala monga chiyambire chilengedwe. Pakuti ichi ayiwala dala, kuti
miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidawungika ndi madzi ndi mwa
madzi, pa Mawu a Mulungu.” (2 Petro 3:3-5).
Mu Mawu Olembedwa omwe ali pamwambawa tikuwona kuti Mulungu mwa
chilungamo amafuna kuti anthu onse apereke kwa Iye ulemerero ndi
kuyamikira zoyenera Iye monga Mlengi wawo; koma munthu wakugwa ali
nacho chifuniro cha kusamvera ndi kuwukira. Chifukwa cha ichi iwo omwe
asiyidwa mu njira zawo zoyipa alibe pokanira. Ndi kudzera mu chisomo
choyenera ndi cha ulere cha Mulungu mwa Khristu Yesu kuti ena
33.
Chitsimikizo cha Ulamuliro Wotsiriza wa Mulungu.
apulumutsidwa, ndi kwa iwo Muwomboli wodalitsika analipira dipo,
anasenza chilango ndi kuwawombola iwo ku chiwerezo. (Aroma 9).
Anthu onse ayenera kufotokoza za moyo wawo kwa Mulungu, ndipo ayenera
kufotokoza za maganizo awo oyipa kwa Iye. Ngakhale tifunafuna kuti tipewe
chowonadi ichi cha ulamuliro wa Mulungu pa miyoyo yathu, sitingapewe
choyikika cha uMulungu wake “Pakuti kwayikika kwa munthu kufa kamodzi
ndipo atafa chiweruzo,” (Ahebri 9:27) “Pakuti ife tonse tidzayima ku mpando
wakuweruza wa Mulungu. Pakuti kwalembedwa. Pali moyo wanga, ati
Ambuye, mabondo onse adzagwadira Ine, ndipo malirime onse
adzavomereza Mulungu. Chotero munthu ali yense wa ife adzadziwerengera
mulandu wake kwa Mulungu.” (Aroma 14:10-12).
Kwa anthu a Ambuye, mulandu uwu pamaso pa Mulungu unakonzedwa
kudzera mu moyo wolungama ndi nsembe yangwiro ya chimo pa Kalvari ndi
Ambuye Yesu Khristu. (Aroma 5 ndi Afilipi 3). Koma timangozitengera kuti ndi
momwe zikhalira kuchimwa pang’ono chifukwa Khristu anatiwombola ife?
Ngati timamukonda mowonadi Iye, ndi zotsimikizika kuti mowona mtima
tikhumba kuti tikhale mfulu ku chimo ndi kulira kamba ka chikhalidwe chathu
cha uchimo ndi machimo omwe anamukhomera Iye ku mtanda. Kapena,
zidzakhala zochititsa mantha kupezeka kuti “tamupondereza Mwana wa
Mulungu” ndipo kenaka “ndi kugwa m’manja mwa Mulungu wamoyo.”
(Ahebri 10:10-31) “Mwa ichi polandira ufumu wosagwedezeka, tikhale nacho
Chisomo, chimene titumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi
kumchitira ulemu ndi mantha. Pakuti Mulungu wathu ndiye moto
wonyeketsa.” (Ahebri 12:28-29).
Kubwera kwa Chiwiri kwa Khristu.
Kubweranso ku dziko la pansi kwa Ambuye Yesu Khristu kudzalengeza za
kutha kwa dziko la pansi (Marko 13:24-31). Dziko iri lidzatha pa nthawi
imeneyi ndipo ndi njira yomwe Mulungu anayikhazikitsa. Sichiri chakuti
munthu angathe kulota kapena mwa kudziwa za kutsogolo mwa nzeru za
munthu; koma ziyenera kulandiridwa mwa chikhulupiriro mogwirizana ndi
Mawu a Mulungu. Dziko siridzatha mwa chifukwa cha zochitika kwa zinthu
pakupita kwa nyengo kwa dziko lonse, kapena siridzatha chifukwa munthu
wapumira mpweya wambiri woturuka mwa iye kupita mlengalenga; koma
34.
Chitsimikizo cha Ulamuliro Wotsisiriza wa Mulungu.
pomwe Khristu adzabwerera mu ulemerero Wake.
Potero ife talamulidwa kuti tikhale tcheru ndi kupempherera kubweranso
kwa Ambuye. “Koma za tsiku ilo, kapena nthawi yake sadziwa munthu,
angakhale angelo m’Mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye.
Yang’anirani, dikirani, pempherani, pakuti simudziwa nthawi yake. Monga
ngati munthu wa pa ulendo, adachoka kunyumba kwake, nawapatsa akapolo
ake ulamuliro, kwa munthu ali yense ntchito yake nalamulira wapakhomo
adikire. Chifukwa chake dikirani; pakuti simudziwa inu nthawi yake
yakubwera mwini nyumba, kapena madzulo, kapena pakati pa usiku, kapena
pakulira tambala, kapena mamawa.” (Marko 13:32-35).
Kubweranso kwa Khristu kudzakumana ndi kukondwerera kwa anthu Ake
owomboledwa , ndi chikondwereronso kumwamba. Kuwonekanso kwake
kudzakhala kwa kugonjetsa adani a Mulungu ndi uMulungu. Ngakhale
atakhala pa mgwirizano mu mphamvu zawo zonse, sadzapambana.
Masomphenya omwe mtumwi Yohane analandira adzakwaniritsidwa
mokhudzana ndi Khristu pa kubwera kwake. Mu masomphenyawo Yohane
anawona kuti Iye “womkera wotchedwa Wokhulupirika ndi Wowona; ndipo
aweruza nachita nkhondo molungama. Ndipo maso ake ali lawi la moto,
ndipo pamutu pake pali nduwira za chifumu zambiri; ndipo ali nalo dzina
lolembedwa, wosalidziwa wina yense koma Iye yekha. Ndipo avala chovala
chowazidwa mwazi; ndipo atchedwa dzina lake Mawu a Mulungu.”
(Chivumbulutso 19:11-13).
Pa kubwera kwa Khristu, monga timawerenga za Iye kuti “adzapereka ufumu
kwa Mulungu, ndiye Atate, atatha kuthera chiweruzo chonse, ndi ulamuliro
wonse ndi mphamvu yomwe. Pakuti Iye ayenera kuchita ufumu kufikira
atayika adani onse pansi pa amapazi ake. Mdani wotsiriza amene adzathedwa
ndiye imfa.” (1 Akorinto 15:24-26). Khristu ali ndi “zofungulira za imfa ndi
hade” ndi “fungulo la Davide,” Iye ali “wotsegula, ndipo palibe wina atseka;
Iye wotseka ndipo palibe wina atsegula. (Chivumbulutso 1:18 ndi 3:7).
Ambuye ali ndi ulamuliro wakuwapititsa anthu ochimwa ku chilango chosatha
amene afa mu machimo awo, ndiponso ali ndi ulamuliro womwewo kuti
atsegule zipata za Yerusalemu wakumwamba kwa iwo omwe ali
owomboledwa ndi mwazi Wake wa mtengo wapatali womwe unakhetsedwa
pa Kalvari. (Mateyu 25:31-46).
35.
Chitsimikizo cha Ulamuliro Wotsiriza wa Mulungu.
Ulamuliro wa Khristu monga Mfumu ya mafumu ndi Ambuye wa ambuye
udzakhala wa muyaya. Ulamuliro wa Mulungu udzakondwereredwa ndi
kutamandidwa ndi onse owomboledwa a Ambuye, adzayika pamaso pa Iye a
korona awo. (Chivumbulutso 4:21 ndi 22). Kwa iwo oyipa ndi osatembenuka
mtima, malo awo adzakhala Nyanja ya moto Chivumbulutso 20 :11-15), “ndi
utsi wa kuzunza kwawo ukwera ku nthawi za nthawi; ndipo sapuma usana ndi
usiku” .(Chivumbulutso 14:11).
Ulamuliro wa Mulungu uyenera kudzafika pa nthawi yakuti utsimikizidwe kwa
muyaya ngakhale mu chiweruzo ndi chowonongeko cha muyaya cha
ochimwa. Koma mpingo wowomboledwa, Mkwatibwi wa Khristu, kwa
muyaya udzakondwera kukhala womasuka ku mphamvu ya chimo, Satana ndi
imfa, ndi kukondwera kuti ayimbe, “Ayenera Mwana wa Nkhosa,
wophedwayo, kulandira chilimbiko, ndi chuma, ndi ulemerero, ndi
chiyamiko.” (Chivumbulutso 5:12). Adzakwera kukhala kwa muyaya pansi pa
ulamuliro wa chikondi ndi wa chisomo wa Mfumu ya mafumu.
Kumaliza.
Tiyenera tsopano kulifikitsa buku laling’onoli ku mapeto. Tafunafuna kuti
tifotokoze za mfundo zazikulu za phunziro lathu, mwa zina zambiri zomwe
zikadakhoza kukambidwa. Baibulo lonse limalankhula za ulamuliro wa
Mulungu kuchokera ku Genesis mpaka ku Chivumbulutso.
Ndiye, wowerenga, tikupemphani kuti mwa pemphero mufufuze Mawu
Olembedwa, kufunafuna chisomo cha Mulungu ndi kuti chithandizo cha
mphamvu yonse cha Mzimu Woyera kukupatsani kuzindikira ndi kuti
muyende mu chowonadi. Monga Ambuye Yesu Khristu anena “Indetu ndidza
msanga. Amen.” Momwenso ife tibwereze pa kunena; “Idzani, Ambuye Yesu”
(Chivumbulutso 22:20).
36.
ULAMULIRO WA MULUNGU.
Buku ili likuwonetsa phunziro pogwiritsa ntchito Baibulo, Mawu a Mulungu,
monga maziko okhawo.
Pamene tingawone ochimwa akukaniza ulamuliro wa Mulungu, buku ili
linalembedwa mwapadera kwa mamembala ndi atumiki a mipingo. Mu
masiku a utumiki wa dziko la pansi wa Ambuye Yesu Khristu, ambiri a anthu
a chipembedzo a masiku amenewo adakaniza ulamuliro Wake ndipo
“sakadafuna munthu uyu kuti awalamulire” iwo.
Mwa tsoka, lero, tikuwona zambiri zofanana ndi zomwezo. Pali mipingo ndi
atumiki omwe sadzagwadira ulamuliro wa Mulungu monga wavumbulutsidwa
mu Mawu a Mulungu, komatu iwo asankha kufunafuna kuti alowetse m’malo
mwake miyambo yawo kapena monga mwa machitidwe a zinthu a dziko la
pansi m’malo mwa chiphunzitso cha uMulungu. Ena anyengedwa mwa
kuchenjera kwa Satana ndipo ali ambiri omwe ali kufunafuna chowonadi
mowona mtima, koma ali ndi mpata wochepa wakuwerenga Baibulo lathunthu
kapena zolembedwa za Mawu a Mulungu zomwe ziri za thunthu. Pa chifukwa
cha ichi ndi chomwe Free Grace Evangelistic Association iri ndi kukhudzidwa
kwa padera.
Buku iri lalembedwa kuti lithandize ndi kulangiza iwo omwe akufunafuna
kuphunzira za Khristu, ndi omwe akukhumba kuchokera pansi pa mtima kuti
alemekeze ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu mu mitima yawo,
m’mipingo ndi utumiki. Lirinso chenjezo, kuti tipemphere kuti tigwiritsidwe
ntchito mwa mphamvu ndi Mulungu kuti tidzutse ena ali wonse womwe ali
mu mdima kapena mu kuwukira.
Dr Ian Sadler (BSc, PhD, DLit) ndi Mtsogoleri wa Mkulu wa Free Grace
Evangelistic Association wa dziko lonse la pansi ndiponso ndi wa pa Mpando
wa Free Grace Evangelistic Association ku Mangalande(Ulaya) komwe ndi ku
Likulu . Amakhala ku Ulaya ndipo ndi mtumiki wa mpingo wa Strict Baptist.
Ali pa banja ndipo ali ndi ana anayi. Analembanso mabuku ena awa:
“Chinsinsicho, Babulo wa Mkulu”, Yesu, ndiye Njira”, ndi “Chikondi cha
Mulungu”.

Documentos relacionados

CHA61-1015M Mafunso ndi Mayankho VGR

CHA61-1015M Mafunso ndi Mayankho VGR anapatukana, ena ankafuna kuti akhalebe ndi Mawu, Mawu olembedwa, ena ankafuna mpingo wapamwamba. Izo zinali mu nthawi ya ulamuliro wa Konstantini. Ndipo Konstantini sanali munthu wachipembedzo; iy...

Leia mais

ubatizo wa mzimu woyera

ubatizo wa mzimu woyera 29 Tsopano, inu mukhoza kutenga chidutswa chaching’ono cha Lemba pano, nkuti, “Yesu anachita zakuti-n-zakuti ndipo ife tiyenera kumachita zomwezo,” inu mukhoza kuwapanga Iwo kunena chirichonse chim...

Leia mais

CTK64-0629 Chiuta Mwenenkhongonozose Kuvumbukwa Kwa Ise

CTK64-0629 Chiuta Mwenenkhongonozose Kuvumbukwa Kwa Ise muzga, ndipo wakapangika mu chikozgo cha ŵanthu: Ndipo pakuti wakawoneka mu kulingana na munthu, wakajiyuyura yekha, ndipo wakazgoka wakupulikira ku nyifwa, nanga ndi nyifwa ya mphinjika.

Leia mais